PHUNZILO 17
Muzikamba Zosavuta Kumvetsa
1 Akorinto 14:9
ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kumvetsa tanthauzo la zimene mukukamba.
MOCITILA:
Iŵelengeni mokwanila nkhani yanu. Muimvetsetse bwino-bwino kuti mukaikambe mosavuta komanso m’mawu anu-anu.
Muzikamba ziganizo zifupi-zifupi na mawu osavuta. Ngakhale kuti ziganizo zazitaliko zili bwino, mveketsani mfundo zofunika mwa kukamba ziganizo zofupikilapo.
Fotokozelani mawu acilendo. Cepetsani mawu acilendo kwa omvela anu. Koma ngati m’pofunika kuti muchule liwu lacilendo, kapena munthu wosadziŵika kwambili wa m’Baibo, muyeso kapena mwambo wamakedzana, fotokozelani.