LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 3
  • Kukoma Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kukoma Mtima
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli
  • Tiphunzilaponji kwa Yesu?
  • Tengelani Citsanzo ca Yesu
  • Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Lolani Kuti “Lamulo la Kukoma Mtima Kosatha” Lizikutsogolelani
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kukoma Mtima Khalidwe Limene Limaonekela M’mawu na M’zocita
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Cifundo
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 3

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Yesu akugwila munthu wakhungu bwino-bwino kuti amucilitse.

Yohane 9:1-7

PHUNZILO 3

Kukoma Mtima

Mfundo Yaikulu: “Cikondi . . . n’cokoma mtima.”—1 Akor. 13:4.

Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli

Yesu akugwila munthu wakhungu bwino-bwino kuti amucilitse.

VIDIYO: Yesu Acilitsa Munthu wa Khungu

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Yohane 9:1-7. Kenaka ganizilani mafunso otsatilawa:

  1. Kodi Yesu anayambila citi—kucilitsa munthu wa khungu, kapena kum’lalikila uthenga wabwino?—Onani Yoh. 9:35-38.

  2. N’cifukwa ciyani njila imeneyi inamufeŵetsa munthuyo kuti amvetsele uthenga wabwino?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Munthu akaona kuti timasamala za iye, amamvetsela uthenga wathu.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Khalani wacifundo kwa munthuyo. Yesani kuganizila mmene munthuyo akumvela.

  1. Dzifunseni kuti: ‘Kodi cikumudetsa nkhawa cingakhale ciyani? Ni mfundo iti ingam’thandize kapena kumukopa cidwi?’ Mukatelo mudzaonetsa cifundo cocokela pansi pa mtima, osati caciphamaso.

  2. Onetsani kuti mumasamala za munthuyo pomumvetsela mwachelu. Ngati iye wakuuzani mmene amaonela nkhani ina yake, kapena wakuchulilani vuto limene ali nalo, musanyalanyaze.

4. Kambani mokoma mtima komanso mwaulemu. Ngati munthuyo mwamumvela cifundo, ndipo mufunadi kum’thandiza, makambidwe anu amaonetsa zimenezo. Sankhani mawu abwino, komanso kambani mokoma mtima. Pewani kukamba zimene zingakhumudwitse munthu.

5. Khalani na mtima wofuna kuthandiza. Pezani njila zimene mungamuthandizile munthuyo. Kuthandizilako anthu pa zinthu zina kumatsegula khomo la makambilano.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma 12:15, 16; Agal. 6:10; Aheb. 13:16

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani