LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 1
  • Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anacitila Zimenezi
  • Tiphunzilaponji kwa Yesu?
  • Tengelani Citsanzo ca Yesu
  • Kukamba Mwacibadwa
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano Otsogolela ku Ulaliki
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano ndi Colinga Cakuti Ticite Ulaliki Wamwai
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kukoma Mtima
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 1

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Yesu akambilana na mzimayi pa citsime.

Yohane 4:6-9

PHUNZILO 1

Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo

Mfundo Yaikulu: “Cikondi . . . sicisamala zofuna zake zokha.”—1 Akor. 13:4, 5.

Mmene Yesu Anacitila Zimenezi

Yesu akambilana na mzimayi pa citsime.

VIDIYO: Yesu na Mzimayi pa Citsime

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Yohane 4:6-9. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Kodi Yesu anazindikila ciyani za mzimayiyu asanayambe kukambilana naye?

  2. Yesu anati: “Mundipatseko madzi akumwa mayi.” N’cifukwa ciyani imeneyi inali njila yaluso yoyambila makambilano?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Nthawi zambili makambilano athu amayenda bwino ngati tiyamba na nkhani imene imam’khudza munthuyo.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Khalani wokonzeka kusintha. Musakhale na maganizo ongofuna kukambilana nkhani imene inuyo mwaikonzekela. Yambani na nkhani imene munthuyo ali nayo m’maganizo lelo. Conco dzifunseni kuti:

  1. ‘Kodi pa nyuzi pamveka nkhani yanji?’

  2. ‘Kodi ni nkhani yanji ili m’kamwa-m’kamwa kwa anthu oyandikana nawo, ku nchito kwathu, kapena ku sukulu?’

4. Khalani oyang’anitsitsa. Dzifunseni kuti:

  1. ‘Kodi munthuyu namupeza akucita ciyani? Kodi mwina akuganiza ciyani?’

  2. ‘Kodi zimene wavala, mmene iye akuonekela, kapena pa nyumba pake, zionetsa kuti ni wacipembedzo canji, kapena ni wa mtundu wanji?’

  3. ‘Kodi ino ni nthawi yabwino yoceza naye?’

5. Muzimvetsela.

  1. Musamafotokoze zambilimbili.

  2. Mulimbikitseni kukambapo maganizo ake. Pa mpata wabwino, m’funseni mafunso.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mat. 7:12; 1 Akor. 9:20-23; Afil. 2:4; Yak. 1:19

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani