LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 September tsa. 8
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano Otsogolela ku Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano Otsogolela ku Ulaliki
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano ndi Colinga Cakuti Ticite Ulaliki Wamwai
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Pezani Cimwemwe Poyambitsa Makambilano
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Kukamba Mwacibadwa
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 September tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano Otsogolela ku Ulaliki

Poyamba na kuceza cabe na mzimayi wacisamariya, Yesu anakwanitsa kucita ulaliki wamwayi. Kodi tinganole bwanji luso lathu loyambitsa makambilano na ŵanthu amene sitiwadziŵa?

Yesu akamba na mzimayi wacisamariya pa citsime
  • Muzikamba na ŵanthu mwaubwenzi. Ngakhale kuti anali atalema, Yesu anayamba kukambilana na mayiyo mwa kungom’pempha madzi akumwa. Conco, mungayambe na moni waubwenzi, kenako n’kukambako za mmene kwacela tsikulo, kapena nkhani ina yake yodziŵika. Kumbukilani kuti, colinga coyamba ni kuyambitsa cabe makambilano. Mungakambe nkhani iliyonse imene munthu angacite nayo cidwi. Ngati sakuyankha, musadandaule. Yesaninso munthu wina. Pemphani Yehova kuti akulimbitseni mtima.—Neh. 2:4; Mac. 4:29.

  • Muziona bwino mpata woloŵetselapo ulaliki, koma osafulumila kwambili. Coyamba cezankoni cabe. Cifukwa ngati mulimbikila zakuti mulalikile, munthuyo adzamangika ndipo angaleke kulankhula. Ngati makambilano atha musanapeze mpata womulalikila, osakhumudwa. Ndipo ngati mumacita mantha kucita ulaliki wamwayi, yesani kumayambitsa makambilano popanda colinga colalikila. [Tambitsani na kukambilana vidiyo yoyamba.]

  • Yesani kupeza poloŵela kuti muyambe kulalikila mwa kukamba zimene mumakhulupilila. Zimenezi zingapangitse munthuyo kukufunsani kuti amve zambili. Yesu anakamba mawu okopa cidwi amene anapangitsa mayi uja kufunsa mafunso. Pamene anayamba kumufotokozela uthenga wabwino, Yesu anali kuyankha mafunso a mayiyo. [Tambitsani na kukambilana vidiyo yaciŵili. Pambuyo pake, tambitsani na kukambilana vidiyo yacitatu.]

Azimayi aŵili acita maseŵela oponyelana bola

Kuyambitsa makambilano kuli monga maseŵela oponyelana bola. Angangofuna anthu aŵili, ndipo ni osavuta kuyamba kuseŵela. Koma mungadziŵe bwanji kuti munthu winayo angakonde kukambilana namwe? “M’ponyeleni” mawu, ndipo onani ngati “adzaŵakha na kukubwezelani.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani