Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano ndi Colinga Cakuti Ticite Ulaliki Wamwai
Cifukwa Cake N’kofunika: Tikamacita ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, tingapeze kuti anthu ena sapezeka pa khomo. Conco tikhoza kulankhula nao tikakwela basi imodzi, tikamayembekezela dokotala, tikamapumula kunchito kapena ku sukulu, kapenanso panthawi ina. Ndi cifunilo ca Yehova kuti anthu onse amve uthenga wa Ufumu. (1 Tim. 2:3, 4) Kuti tilalikile anthu, nthawi zambili ndife amene tifunika kuyamba makambilano.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Yesani kuyambitsa makambilano mwina kamodzi mlungu uliwonse ndi colinga cakuti mucite ulaliki wamwai.