CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOHANE 3-4
Yesu Alalikila Mayi Wacisamariya
N’ciani cinathandiza Yesu kucita ulaliki wamwayi?
4:7—Iye anayambitsa makambilano mwa kupempha madzi akumwa m’malo mokamba za Ufumu, kapena kudziulula kuti ni Mesiya
4:9—Iye sanaweluziletu mayi wacisamariya cifukwa ca mtundu wake
4:9, 12—Pamene mayiyo anayambitsa nkhani zofuna kubweletsa mkangano, Yesu sanapatuke pa mfundo imene anali kuifotokoza.—cf peji 77 pala. 3
4:10—Iye anayambitsa makambilano ake mwa kuseŵenzetsa cinthu codziŵika kwa mayiyo
4:16-19—Yesu anakamba na mayiyo mwaulemu olo kuti anali kukhala umoyo waciwelewele
Kodi nkhaniyi ionetsa bwanji kufunika kocita ulaliki wamwayi?