LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 9
  • Cifundo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cifundo
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli
  • Tiphunzilaponji kwa Yesu?
  • Tengelani Citsanzo ca Yesu
  • Onetsani Cifundo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Onetsani Cifundo
    Galamuka!—2020
  • Kukoma Mtima
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Kodi Mulungu Ni Wacifundo Zoona?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 9

KUBWELELAKO

Yesu na ophunzila ake atsika m’boti akupita ku khamu la anthu omwe akuwayembekezela m’mphepete mwa nyanja.

Maliko 6:30-34

PHUNZILO 9

Cifundo

Mfundo Yaikulu: “Sangalalani ndi anthu amene akusangalala. Lilani ndi anthu amene akulila.”—Aroma 12:15.

Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli

Yesu na ophunzila ake atsika m’boti akupita ku khamu la anthu omwe akuwayembekezela m’mphepete mwa nyanja.

VIDIYO: Yesu Amvela Cifundo Khamu la Anthu

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Maliko 6:30-34. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. N’cifukwa ciyani Yesu na atumwi ake anafuna “kupita kwaokhaokha ku malo opanda anthu”?

  2. N’ciyani cinapangitsa Yesu kuti awaphunzitsebe anthuwo?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Cifundo cimatipangitsa kuwaganizila anthu, osati kungoganiza za uthenga wathu cabe.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Muzimvetsela mosamala. Lolani munthuyo akambe maganizo ake momasuka. Musam’dule mawu, ndiponso musangoponya ku nkhongo zimene wakamba, maganizo ake, nkhawa zake, kapena mfundo zake zotsutsa. Pomumvetsela mwachelu, mumaonetsa kuti mufunadi kumvetsa maganizo ake.

4. Sinkhasinkhani za munthu wacidwiyo. Malinga ni zimene mwakambilanapo naye, dzifunseni kuti:

  1. ‘N’cifukwa ninji munthu uyu afunikiladi kumva coonadi?’

  2. ‘Kodi kuphunzila Baibo kungam’pindulile bwanji pa umoyo wake wa tsiku na tsiku, kutinso akhale na tsogolo labwino?’

5. Kambilanani naye zinthu zimene zingam’thandizedi pa umoyo wake. Pasanapite nthawi yaitali, muonetseni mmene phunzilo la Baibo lingayankhile mafunso ake, na mmene lingam’pindulile pa umoyo wake.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma 10:13, 14; Afil. 2:3, 4; 1 Pet. 3:8

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani