LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 8
  • Kuleza Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuleza Mtima
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli
  • Tiphunzilaponji kwa Yesu?
  • Tengelani Citsanzo ca Yesu
  • Khalanibe Oleza Mtima
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mavidiyo Pophunzitsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Pindulani na Nsembe ya Yesu
    Nkhani Zina
  • Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 8

KUBWELELAKO

Yesu afikila m’bale wake Yakobo m’cipinda cogwilila nchito ya ukalipentala. Yakobo akudabwa kumuona.

Yohane 7:3-5; 1 Akor. 15:3, 4, 7

PHUNZILO 8

Kuleza Mtima

Mfundo Yaikulu: “Cikondi n’coleza mtima.”—1 Akor. 13:4.

Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli

Yesu afikila m’bale wake Yakobo m’cipinda cogwilila nchito ya ukalipentala. Yakobo akudabwa kumuona.

VIDIYO: Yesu Athandiza M’bale Wake Moleza Mtima

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Yohane 7:3-5 na 1 Akorinto 15:3, 4, 7. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Kodi poyamba abale a Yesu anacita motani atamva uthenga wake?

  2. N’ciyani cionetsa kuti Yesu sanataye mtima pothandiza m’bale wake Yakobo?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Tizikhala oleza mtima cifukwa anthu ena amatenga nthawi yotalikilapo kuti alabadile uthenga wabwino.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Yesani njila ina. Ngati poyamba munthu wakana phunzilo la Baibo, musamuumilize. Pa nthawi yoyenela, muonetseni mavidiyo kapena nkhani zina zomuthandiza kudziŵa mmene phunzilo la Baibo limacitikila, komanso mmene iye angapindulile.

4. Musayelekezele anthu. Munthu aliyense ni wosiyana. Ngati wina m’banja, kapena munthu pa ulendo wobwelelako azengeleza kuphunzila Baibo, kapena kuvolemeleza mfundo inayake ya m’Baibo, ganizilani cingakhale cifukwa cake. Kodi pali zimene amakhulupilila zomwe n’zofunika kwambili kwa iye? Kodi n’cifukwa ca cipembedzo cake? Kodi n’kutheka acibale ake, kapena maneba ake, ni amene amamuopseza? M’patseni nthawi yoti aganizilepo pa mfundo zimene mwamuuzapo, kutinso aone phindu la zimene Baibo imanena.

5. M’pempheleleni munthu wacidwi. Pemphani Yehova akuthandizeni kukhala wacidalilo komabe wosamala. M’pempheninso akuthandizeni kuzindikila pamene muyenela kungomusiya munthu wopanda cidwi ceniceni.—1 Akor. 9:26.

ONANINSO MALEMBA AWA

Maliko 4:26-28; 1 Akor. 3:5-9; 2 Pet. 3:9

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani