LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 7
  • Khama

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Khama
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Paulo Anaonetsela Khalidwe Limeneli
  • Tiphunzilaponji kwa Paulo?
  • Tengelani Citsanzo ca Paulo
  • Kudzicepetsa
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Kuleza Mtima
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Kodi Mumaona Kufunika Kophunzitsa Ena?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 7

KUBWELELAKO

Mtumwi Paulo akulalikila uthenga wabwino ku gulu la anthu mu holo pa sukulu.

Machitidwe 19:8-10

PHUNZILO 7

Khama

Mfundo Yaikulu: “Anapitiliza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.”—Mac. 5:42.

Mmene Paulo Anaonetsela Khalidwe Limeneli

Mtumwi Paulo akulalikila uthenga wabwino ku gulu la anthu mu holo pa sukulu.

VIDIYO: Paulo Acita khama ku Efeso

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Machitidwe 19:8-10. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. M’malo mokhwethemuka cifukwa ca anthu omutsutsa, kodi Paulo anacita bwanji kuti awathandizebe anthu acidwi?

  2. Kodi Paulo anabwelelako kangati kuti akaphunzitse anthu acidwi, ndipo anacita zimenezi kwa utali wotani?

Tiphunzilaponji kwa Paulo?

2. Kuti tipange maulendo obwelelako ofika pamtima, na kuyambitsa maphunzilo a Baibo, tiyenela kutayilapo nthawi komanso kucita khama.

Tengelani Citsanzo ca Paulo

3. Sankhani tsiku lokomela munthuyo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi iye amapeza liti mpata wabwino, ndipo nthawi yanji? Nanga angakonde nizicezela naye kuti?’ Yesetsani kubwelelako ngakhale pamene si nthawi yabwino kwa inu.

4. Panganani pasadakhale. Nthawi zonse mukamaliza makambilano anu, panganani za tsiku na nthawi pamene mudzacezenso. Yesetsani kusunga cipangano.

5. Khalanibe na cidalilo. Musafulumile kuganiza kuti munthuyo alibe cidwi cabe cifukwa sapezeka-pezeka pa nyumba, kapena amakhala wotangwanika kwambili. (1 Akor. 13: 4, 7) Ngakhale n’telo, samalani nawo anthu amene angangokutayilani nthawi.—1 Akor. 9:26.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mac. 10:42; 1 Akor. 9:22, 23; 2 Akor. 4:1; Agal. 6:9

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani