LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 1 masa. 5-6
  • Mungacite Ciani Kuti Kuŵelenga Baibo Kuzikukondweletsani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mungacite Ciani Kuti Kuŵelenga Baibo Kuzikukondweletsani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Nkhani Zofanana
  • Ndani Anagaŵa Baibulo Kuti Likhale Ndi Macaputala Ndi Mavesi?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Zimene Mungacite Kuti Muzipindula Kwambili Poŵelenga Baibo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Buku Losavuta Kumvetsetsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 1 masa. 5-6
Mkazi aseŵenzetsa zida zothandiza pophunzila Baibo pamene akuiŵelenga

NKHANI YA PACIKUTO MUNGACITE CIANI KUTI MUPINDULE NA ZIMENE MUŴELENGA M’BAIBO?

Mungacite Ciani Kuti Kuŵelenga Baibo Kuzikukondweletsani?

Kodi mumakondwela pamene muŵelenga Baibo kapena simukondwela? Kuti muzikondwela, zimadalila mmene mumaiŵelengela. Onani zimene mungacite kuti muzikonda kuŵelenga Baibo ndi kuti muzikondwela pamene muŵelenga.

Sankhani Baibo yodalilika ndi ya mau osavuta kumva. Ngati muŵelenga Baibo imene ili na mau ambili ovuta kumva, acikale, kapena amene simuwadziŵa, simungakondwele poiŵelenga. Conco, sankhani Baibo imene muli mau osavuta kumva amene angakufikeni pamtima. Komanso iyenela kukhala yomasulidwa molongosoka.a

Muziseŵenzetsa zipangizo zamakono. Masiku ano, Baibo siipezeka cabe monga buku lopulintiwa, koma imapezekanso pa kompyuta. Mabaibo ena mukhoza kuwaŵelengela pa intaneti kapena mungacite daunilodi kuti muziwaŵelengela pa kompyuta, pa tabuleti, kapena pa foni yanu. Mabaibo ena ali na zinthu zimene zingakuthandizeni kuyelekezela mavesi amene muŵelenga ndi mavesi ena a m’Baibo, kapena kuyelekezela mmene Mabaibo ena anamasulila mavesiwo. Ngati simufuna kucita kuŵelenga Baibo, mungamvetsele mau a m’Baibo ojambulidwa. Anthu ambili amakonda kumvetsela nyimbo ndi zinthu zina poyenda, powacha, kapena pocita zinthu zina. Kodi inu mungayeseko kumvetsela Baibo pocita zina mwa zinthu tachulazi?

Muziseŵenzetsa zida zothandiza pophunzila Baibo. Zida zothandiza pophunzila Baibo zingakuthandizeni kumvetsetsa zimene muŵelenga. Pali mamapu oonetsa malo a m’Baibo amene angakuthandizeni kudziŵa malo ochulidwa m’Baibo ndi kumvetsetsa nkhani zimene muŵelenga. Komanso nkhani za m’magazini ino kapena zopezeka pa webusaiti ya jw.org, pa cigawo cakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa,” zingakuthandizeni kumvetsetsa tanthauzo la malemba ambili.

Muzisintha-sintha kaŵelengedwe kanu. Ngati muona kuti kuŵelenga Baibo kucokela kuciyambi mpaka kumapeto n’kocititsa ulesi, mungayambile kuŵelenga nkhani zimene zimakukondweletsani ngako. Ngati mufuna kudziŵa bwino anthu ochulidwa m’Baibo, mungayese kuiphunzila motsatila maina a anthu a m’Baibo. Njila imeneyi yaonetsedwa m’bokosi yakuti “Phunzilani za Anthu Ochulidwa m’Baibo Kuti Muimvetsetse.” Komanso ngati mufuna, mungaŵelenge Baibo motsatila mitu ya nkhani kapena motsatila ndondomeko ya mmene zinthu zinacitikila. Kodi mungayeseko kucita zimenezi?

a Anthu ambili aona kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ni lolongosoka, lodalilika, ndi losavuta kumva. Baibo imeneyi ni yomasulidwa na Mboni za Yehova, ndipo ipezeka m’zitundu zoposa 130. Mungacite daunilodi Baibo imeneyi pa webusaiti ya jw.org kapena mungacite daunilodi JW Library. Ndipo ngati mufuna, mungapemphe a Mboni za Yehova kuti akubweletseleni Baibo kunyumba kwanu.

PHUNZILANI ZA ANTHU OCHULIDWA BAIBO KUTI MUIMVETSETSE

Akazi ena okhulupilika

Abigayeli

1 Samueli caputa 25

Esitere

Esitere caputa 2-5, 7-9

Hana

1 Samueli caputa 1-2

Mariya

(Mayi a Yesu) Mateyu caputa 1-2; Luka caputa 1-2; onaninso Yohane 2:1-12; Machitidwe 1:12-14; 2:1-4

Rahabi

Yoswa caputa 2, 6; onaninso Aheberi 11:30, 31; Yakobo 2:24-26

Rabeka

Genesis caputa 24-27

Sara

Genesis caputa 17-18, 20-21, 23; onaninso Aheberi 11:11; 1 Petulo 3:1-6

Amuna Odziŵika Bwino

Abulahamu

Genesis caputa 11-24; onaninso 25:1-11

Davide

1 Samueli caputa 16-30; 2 Samueli caputa 1-24; 1 Mafumu caputa 1-2

Yesu

Uthenga Wabwino wa Mateyu, Maliko, Luka, na Yohane

Mose

Ekisodo caputa 2-20, 24, 32-34; Numeri caputa 11-17, 20-21, 27, 31; Deuteronomo caputa 34

Nowa

Genesis caputa 5-9

Paulo

Machitidwe caputa 7-9, 13-28

Petulo

Mateyu caputa 4, 10, 14, 16-17, 26; Machitidwe caputa 1-5, 8-12

ZIDA ZOPHUNZILILA BAIBO ZOKONZEDWA NA MBONI ZA YEHOVA

  • JW.ORG—Pa webusaiti imeneyi pali zida zambili zophunzilila, kuphatikizapo nkhani za pa cigawo cakuti “Kuyankha Mafunso a m’Baibulo.” Palinso malangizo a mmene mungacitile daunilodi JW Laibulale

  • “Onani Dziko Lokoma”—M’kabuku kameneka muli mapu na zithunzi za malo ochulidwa m’Baibo

  • Insight on the Scriptures—Buku limeneli lili na zigawo ziŵili, ndipo limafotokoza za anthu, malo, na mau opezeka m’Baibo

  • “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial”—Buku limeneli lili na mfundo zimene zinafufuzidwa mosamala. Limafotokoza nthawi na malo kumene mabuku a m’Baibo analembedwela ndiponso cifukwa cake buku lililonse linalembedwa. Limafotokozanso mwacidule mfundo za m’buku lililonse la m’Baibo

  • Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?—Buku limeneli n’laling’ono koma lili na mfundo zimene zinafufuzidwa mosamala, ndipo limafotokoza umboni woonetsa kuti Baibo ni Mau a Mulungu ouzilidwa

  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?—Aka ni kabuku ka mapeji 32 kamene kamafotokoza mwacidule mfundo yaikulu ya m’Baibo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani