Kuona Zolakwa Moyenelela
Don na Margareta anasangalala kwambili pamene mwana wawo wamkazi na banja lake anawacezela. Ndiyeno, Margaret amene anali katswili wodziŵa kuphika, anakonza zakuti aphike makaloni na chizi monga cakudya colaililana, cakudya cimene adzukulu awo aŵili amacikonda kwambili.
Onse lomba anali atakhala ku thebulo, kuyembekezela cakudya. Margaret anabweletsa cakudya na kuciika pa thebo. Pamene anacotsapo civundikilo pa poto, anadabwa ataona kuti munali cabe supu ya chizi. Margaret anaiŵala kuikamo makaloni, amene ndiye cinali cakudya ceni-ceni!b
Kaya tili na zaka zingati, kapena luso labwanji, tonse timalakwitsa. Tingakambe mosaganiza bwino kapena kucita zinthu panthawi yolakwika. Mwina tinganyalanyaze zinazake kapena kuiŵala. N’cifukwa ciani timalakwitsa? Nanga tingacite ciani tikalakwitsa? Kodi tingakupewe? Kuona zolakwa moyenela kudzatithandiza kuyankha mafunso amenewa.
ZOLAKWA—MMENE TIMAZIONELA NA MMENE MULUNGU AMAZIONELA
Tikacita cinthu cabwino, timakondwela anthu akatiyamikila ndipo timaona kuti n’zoyenelela. Mofananamo, tikalakwitsa, kaya sitinacitile dala kapena ena sanazindikile, kodi sitiyenela kuvomeleza kuti talakwa? Kucita zimenezo kumafuna kudzicepetsa.
Ngati timadziganizila kuposa mmene tiyenela kudziganizila, tingayambe kucepetsa colakwaco, kuimba mlandu ena, kapena kukana kuti ndife tacita. Kucita zimenezo kumabweletsa mavuto. Mwacitsanzo, vuto singasile, ndipo anthu ena osalakwa angaimbidwe mlandu. Olo kuti zinthu zingatiyendele bwino cifukwa cokana kuvomeleza colakwa cathu, tifunika kukumbukila kuti pothela pake, “aliyense wa ife adzadziŵelengela mlandu wake kwa Mulungu.”—Aroma 14:12.
Mulungu amaona zolakwa moyenela. M’buku la Masalimo, Mulungu akunenedwa kuti ni “wacifundo ndi wacisomo.” Iye “sadzakhalila kutiimba mlandu nthawi zonse cifukwa ca zolakwa zathu, kapena kutisungila mkwiyo mpaka kalekale.” Amadziŵa kuti anthu ni opanda ungwilo ndipo amamvetsetsa zofooka zathu, “amakumbukila kuti ndife fumbi.”—Salimo 103:8, 9, 14.
Kuwonjezela apo, monga tate wacifundo, Mulungu afuna kuti ise ana ake, tiziona zolakwa mmene iye amazionela. (Salimo 130:3) Kupitila m’Mau ake, iye amatipatsa malangizo ambili acikondi na citsogozo kuti atithandize kudziŵa zimene tingacite tikalakwa kapena ngati ena alakwa.
ZIMENE TINGACITE TIKALAKWITSA ZINTHU
Kambili munthu akalakwa, amathela nthawi yaitali kuimba ena milandu, kapena kulungamitsa zimene zinakambidwa kapena kucitika. Komabe, ngati mau anu akhumudwitsa ena, bwanji osangopepesa, kukonza zinthu, na kupitiliza kusunga ubwenzi wanu? Kodi munalakwitsa cinacake cimene cabweletsa msokonezo kwa imwe kapena kwa anthu ena? M’malo modziimba mlandu kapena kunamizila ena, bwanji osangocita zilizonse zotheka na kukonza zinthu? Kupatsa ena mlandu kumangobweletsa msokonezo na kukulitsa nkhani. M’malomwake, tengamponi phunzilo, konzani zinthu, na kucita zoyenela.
Koma ngati wina walakwa, cimakhala capafupi kucita zinthu zoonetsa kukhumudwa. Bwanji osatsatila uphungu wa Yesu Khristu wakuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.” (Mateyu 7:12) Mukalakwa, olo kuti colakwaco n’cacing’ono, mumafuna kuti anthu akucitileni zinthu mwacikondi kapena kunyalanyaza colakwaco. Conco bwanji osayesetsa kukomela mtima ena mwa njila imeneyo?—Aefeso 4:32.
MFUNDO ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUTI TISAMALAKWITSE KAŴILI-KAŴILI
Dikishonale ina inafotokoza kuti; zolakwa zimabuka cifukwa ca “kuganiza molakwika, kusadziŵa zonse, kapena kusamvetsela.” Tonse tingavomeleze kuti panthawi ina, munthu aliyense anaonetsapo ena mwa makhalidwe amenewa. Ngakhale n’conco, zolakwa zimacepa ngati tiganizila mfundo zofunika kwambili za m’Malemba.
Mfundo imodzi ili pa Miyambo 18:13, imene imati: “Munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amacita manyazi.” Inde, kupatula nthawi yomvetsela nkhani yonse na kuona zimene mungayankhepo kudzakuthandizani kusayankha mopupuluma kapena kucita zinthu mosaganiza bwino. Kumvetsela mwachelu na kudziŵa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo kungakhale kothandiza kwambili kuti tipewe kuganizila ena molakwa ndi kupewa kulakwitsa zinthu.
Mfundo ina ya m’Baibo imati: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendele ndi anthu onse, monga mmene mungathele.” (Aroma 12:18) Citani zonse zimene mungathe kuti mulimbikitse mtendele na mgwilizano. Poseŵenza ndi ena, khalani woganizila ena ndi waulemu ndipo yesetsani kuwayamikila na kuwalimbikitsa. Mukacita zimenezi, zimakhala zosavuta kukhululuka kapena kunyalanyaza ngati wina wakamba kapena kucita zinthu mosaganiza bwino. Kuwonjezela apo, zolakwa zikulu-zikulu zingathetsedwe mosavuta.
Yesetsani kuona zimene mungaphunzilepo pa zimene mwalakwitsa. M’malo mopeza zifukwa zodzikhululukila pa zimene munakamba kapena kucita, uoneni kukhala mwayi wanu wokulitsa makhalidwe abwino. Kodi mufunika kukhala woleza mtima, wokoma mtima, kapena wodziletsa? Nanga bwanji za kufatsa, mtendele, na cikondi? (Agalatiya 5:22, 23) Ndipo mungaphunzile zimene simuyenela kucita ulendo wotsatila. Yesetsani kusaganizila kwambili mmene zakukhudzilani. Kukhala wansangala kungakuthandizeni kucepetsa nkhawa.
KUONA ZINTHU MOYENELELA KUMAPINDULITSA
Kuona zolakwa moyenelela kudzatithandiza kuthana nazo bwino ngati zacitika. Tidzakhala na mtendele wa m’maganizo ndipo tidzakhalanso pamtendele na ena. Ngati tiyesetsa kuphunzilapo kanthu pa zolakwa zathu, tidzakhala anzelu ndipo anthu adzatikonda. Sitidzakhala na nkhawa kwambili kapena kudziimba mlandu. Kukumbukila kuti anthu ena nawonso akulimbana na zofooka zawo kudzatithandiza kukhala nawo paubwenzi. Koposa zonse, tingapindule ngati titengela cikondi ca Mulungu na kukhululukila ena na mtima wonse.—Akolose 3:13.
Kodi zimene Margaret analakwitsa kuciyambi kwa nkhani ino, zinasokoneza maceza awo a banja? Ayi ndithu. Onse anangoziona ngati zoseketsa, maka-maka Margaret, ndipo onse anadya zakudyazo popanda makaloni. Patapita zaka zambili, adzukulu a Margaret aŵili, anasimbilako ana awo za cakudya ca banja cosaiŵalikaco. Anawauzanso zinthu zabwino zokhudza ambuye awo. Kumbukilani kuti anangolakwitsa cabe!
a Maina ena tawasintha.
b Makaloni na chizi ni cakudya cimene amakonza mwa kuphika makaloni na kuwasakaniza na supu ya chizi.