Nchito Yapadela Imene Imakhala ndi Zotulukapo Zabwino
Milungu itatu msonkhano wa cigawo ukalibe kuyamba, mipingo idzakhala ndi nchito yapadela yoitanila anthu a m’gawo lao kuti akapezekepo pa msonkhano wa cigawo. Pali cifukwa cabwino cokhalila ndi nchito yapadela yapacaka imeneyi. Kaŵili-kaŵili anthu amene amabwela ku msonkhano akaitanidwa amasangalala ndi nkhani za m’Malemba, dongosolo labwino la madipatimenti osiyana-siyana okhala ndi anchito odzifunila, komanso kuona khalidwe labwino ndi mgwilizano umene timakhala nao. (Sal. 110:3; 133:1; Yes. 65:13, 14) Ngakhale n’conco, kodi nchito yathu yapadela imakhala ndi zotsatilapo zabwino, maka-maka ku malo kumene anthu acidwi amayenela kuyenda mitunda yaitali kuti apezeke pa msonkhano?
Pambuyo pa msonkhano wa cigawo wa 2011, ofesi ya nthambi inalandila kalata yocokela kwa mai wina amene anapeza kapepala ka ciitano pa khomo lake. Nthawi zambili anali kubisala Mboni za Yehova zikamagogoda. Iye analemba kuti: “Ndinali ndi nyumba yokongola, mwamuna wabwino, conco ndinaganiza kuti ndinali ndi zinthu zonse zimene zikanandikondweletsa. Koma comvetsa cisoni n’cakuti sindinali wokondwela, ndipo moyo wanga unali wopanda tanthauzo. Conco ndinaganiza zoyenda ulendo wa makilomita 320 kuti ndikapezeke pa msonkhano pa Ciŵelu.” Anasangalala kwambili ndi msonkhano cakuti anatumila foni mwamuna wake kuti sadzabwelela kunyumba n’colinga cakuti akapezekepo pa pulogalamu ya pa Sondo. Anapitiliza kunena kuti, “Ndinamvetsela nkhani zonse, ndipo ndinadziŵa Mboni za Yehova zambili, ndiponso ndinatsimikiza mtima kuti zonse sizidzathela pamenepa.” Pamene anabwelela kunyumba, anayamba kuphunzila Baibo ndipo pambuyo pa miyezi inai anakhala wofalitsa wosabatizika. Ananenanso kuti, “Ndine wosangalala kwambili kuti ndinapeza kapepala ka ciitano pakhomo cifukwa moyo wanga tsopano wakhala ndi tanthauzo leni-leni!”
Ena amene adzalandila kapepala ka ciitano adzapezeka pa msonkhano. Conco, tiyeni ticite cangu kutengako mbali m’nchito yofunika iyi. Ngati tumapepala twa ciitano tudzatsala, mungabwele nato ku malo kumene mudzakhala ndi msonkhano n’colinga cakuti mukacite ulaliki wamwai.
[Bokosi papeji 1]
Kodi Tidzagaŵila Bwanji Kapepala ka Ciitano?
Kuti tikwanitse kufola gawo lathu lonse, tiyenela kukamba mwacidule. Tinganene kuti: Muli bwanji? Tikupatsa anthu padziko lonse tumapepala twa ciitano utu. Ndingakonde kukupatsankoni aka. Mudzapeza mfundo zambili pa kapepalaka.” Khalani wacimwemwe. Pogaŵila tumapepala twa ciitano pa Ciŵelu ndi Sondo, tiyenelanso kugaŵila magazini ngati n’kotheka.