Ciitano Capadela
1. Kodi tidzayamba liti kuitanila anthu ku misonkhano ya cigawo ya 2014?
1 Mukafuna kuitana anzanu kapena banja ku cakudya capadela cimene munafunika kuthelapo mphamvu ndi ndalama, mwacionekele mudzakhala okondwela powaitana. Mofananamo, nchito yaikulu yagwilika pokonzekela cakudya ca kuuzimu cimene tidzadya pa msonkhano wa cigawo ndi wa maiko wa 2014. Pakadzangotsala milungu itatu msonkhano usanayambe, tidzapatsidwa mwai woitanila anthu kuti akapezekepo. Nanga n’ciani cingatithandize kuitanila anthu mwa cangu?
2. N’ciani cidzaticititsa kutengako mbali mokwanila m’nchito yapadela yoitanila anthu ku msonkhano wa cigawo?
2 Tidzalimbikitsidwa kutengako mbali mokwanila m’nchito yapadela ngati tiganizila mmene ifeyo timapindulila ndi cakudya ca kuuzimu cimene Yehova amapeleka pa misonkhano ya cigawo. (Yes. 65:13, 14) Tiyenelanso kukumbukila kuti nchito yoitanila anthu imeneyi imakhala ndi zotsatilapo. Anthu ena amene tidzaitana adzacita nafe msonkhano. Komabe, mosasamala kanthu za ciŵelengelo ca anthu amene adzabwela, khama lathu pocita nchito yapadela imeneyi lidzacititsa kuti Yehova atamandidwe ndi kuonetsa kuolowa manja kwake.—Sal. 145:3, 7; Chiv. 22:17.
3. Tidzagaŵila bwanji tumapepala toitanila anthu?
3 Bungwe lililonse la akulu lingaone mmene mpingo ungagwilile nchito kuti anthu ambili alandile ciitano. Zimenezi zikuphatikizapo kuona ngati n’zotheka kusiya kapepala ka ciitano pa nyumba pamene sitinapeze anthu kapena kutugaŵila pocita ulaliki wapoyela m’gawo lathu. Pamapeto a mlungu, tingagaŵile kapepala ka ciitano pamodzi ndi magazini ngati n’koyenela kutelo. Ngati Ciŵelu coyamba ca mwezi cidzakhalako pa madeti amene tikucita nchito yapadela, tiyenela kuika mtima kwambili pa kugaŵila tumapepala toitanila anthu m’malo mwa kuyambitsa maphunzilo a Baibulo. Nchito yapadela ikadzatha, tidzakhala okondwela kwambili kudziŵa kuti tinatengako mbali mwacangu ndipo tinaitanila anthu ambili kuti adzacite nafe phwando la kuuzimu limene Yehova watikonzela.