LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 6/15 tsa. 4
  • Ciitano Cacindunji

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ciitano Cacindunji
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Ciitano Capadela
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nchito Yapadela Imene Imakhala ndi Zotulukapo Zabwino
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nchito Yogaŵila Tumapepala Toitanila Anthu ku Msonkhano Wacigawo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nchito Yoitanila Anthu ku Cikumbutso Idzayamba pa March 1
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 6/15 tsa. 4

Ciitano Cacindunji

1. Kodi tidzayamba liti kuitanila anthu ku msonkhano wa cigawo?

1 Mukafuna kuitana anzanu kapena banja ku cakudya capadela cimene munafunika kuthelapo mphamvu ndi ndalama, mwacionekele mudzakhala okondwela powaitana. Mofananamo, nchito yaikulu yagwilika pokonzekela cakudya ca kuuzimu cimene tidzadya pa msonkhano wa cigawo. Pakadzangotsala milungu itatu msonkhano usanayambe, tidzapatsidwa mwai woitanila anthu kuti akapezekepo. Nanga n’ciani cingatithandize kuitanila anthu mwacangu?

2. N’ciani cidzaticititsa kutengako mbali mokwanila m’nchito yapadela yoitanila anthu ku msonkhano wa cigawo?

2 Tidzalimbikitsidwa kutengako mbali mokwanila m’nchito yapadela ngati tiganizila mmene ifeyo timapindulila ndi cakudya ca kuuzimu cimene Yehova amapeleka pa misonkhano ya cigawo. (Yes. 65:13, 14) Tiyenelanso kukumbukila kuti nchito yoitanila anthu imeneyi imakhala ndi zotsatilapo. (Onani bokosi lakuti “Pamakhala Zotsatilapo Zabwino.”) Anthu ena amene tidzaitana adzacita nafe msonkhano. Komabe, mosasamala kanthu za ciŵelengelo ca anthu amene adzabwela, khama lathu pocita nchito yapadela imeneyi lidzacititsa kuti Yehova atamandidwe ndi kuonetsa kuolowa manja kwake.—Sal. 145:3, 7; Chiv. 22:17.

3. Tidzagaŵila bwanji tumapepala toitanila anthu?

3 Bungwe lililonse la akulu lingaone mmene mpingo ungagwilile nchito kuti anthu ambili alandile ciitano. Zimenezi zikuphatikizapo kuona ngati n’zotheka kusiya kapepala ka ciitano pa nyumba pamene sitinapeze anthu kapena kutugaŵila pocita ulaliki wapoyela m’gawo lathu. Pamapeto a mlungu, tingagaŵile kapepala ka ciitano pamodzi ndi magazini ngati n’koyenela kutelo. Nchito yapadela ikadzatha, tidzakhala okondwela kwambili kudziŵa kuti tinatengako mbali mwacangu ndipo tinaitanila anthu ambili kuti adzacite nafe phwando la kuuzimu limene Yehova watikonzela.

Kodi Mudzakamba Ciani?

Mukapatsana moni, mungakambe kuti: “Tikugwila nchito yapadela imene ikucitika padziko lonse yoitanila anthu ku cocitika cofunika kwambili. Deti, nthawi ndi malo zalembedwa pa kapepala aka ka ciitano.”

“Pamakhala Zotsatilapo Zabwino”

  • Papita zaka zingapo pamene mlongo wina anali kugaŵila kapepala ka ciitano. Iye anali kuona kuti nchito imene wagwila siidzaphula kanthu. Mlongoyo anadzifunsa kuti: ‘Kodi anthu adzabweladi ku msonkhano?’ Pa Ciŵelu mmaŵa, anaona mwamuna wina wacipembedzo ca Cihindu ali khale pafupi ndi iye pa msonkhanowo. Conco iye anadzidziŵikitsa kwa munthuyo. Mlongoyo anazindikila kuti munthuyo anali pa msonkhonopo cifukwa cakuti anali atalandila kapepala ka ciitano. Mwamunayo anafunsa mafunso ambili amene mlongoyo anayankha. Mwamunayo anafotokoza mmene anapindulila ndi msonkhano ndipo anakamba kuti anacita cidwi ndi kaonekedwe ndiponso khalidwe la abale ndi alongo. Tsiku limodzimodzilo, mlongoyo anacezanso ndi banja lina limene linali pafupi ndi iye. Banjalo linalandila kapepala ka ciitano ndipo linacita kubwela ndi galimoto. Iwo anasangalala kwambili ndi msonkhano ndipo anaganiza zodzapezekanso pa Sondo. Conco mlongo wathu anazindikila kufunika kwa kuitanila anthu kumisonkhano ya pacaka.

  • Pa msonkhano waposacedwapa mwamuna ndi mkazi wake amene ndi apainiya anaceza ndi banja lina lacikulile limene linapezeka pa msonkhano. Banjalo linafotokoza kuti kanali koyamba kupezeka pa msonkhano. Apainiyawo anafunsa kuti: “Ndani anakuitanani?” Banjalo linayankha kuti “tinapeza kapepala ka ciitano pa nkhomo la nyumba yathu.” Iwo anaŵelenga kapepalako ndi kudzadza danga limene lili pa tsamba lothela la kapela ka ciitano. Ndipo abale ndi alongo ena anadya nao cakudya camasama. Iwo anakambanso kuti anasangalala kwambili ndi msonkhano tsikulo, ndipo anaganiza zodzapezekanso tsiku lotsatila. Makonzedwe anapangidwa akuti akawafikile ku nyumba kwao.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani