Khalidwe Limene Limalemekeza Mulungu
1. N’cifukwa ciani n’zosavuta kwa anthu kudziŵa kuti Mboni za Yehova zili ndi misonkhano ya cigawo?
1 N’zosavuta kwa anthu kudziŵa kuti tili ndi misonkhano ya cigawo. M’mizinda yambili mmene muli misonkhano ya cigawo, amtolankhani amadziŵitsa anthu a kumaloko za misonkhano yathu. Mahotelo ndi malesitilanti kaŵili-kaŵili amadzaza ndi alendo, ndipo anthu amene akhala kumalo kumeneko amaona alendo ambili atavala mabaji a msonkhano. Mfundo zotsatilazi ndi zikumbutso zimene zidzatithandiza kuti tilemekeze Mulungu mwa kukhala ndi khalidwe labwino pamene tili ku malo a msonkhano.—1 Pet. 2:12.
2. Kodi tingalemekeze bwanji Mulungu mwa kavalidwe kathu pamene tili pa malo a msonkhano?
2 Kavalidwe Koyenela: Kavalidwe kathu koyenela pamene tili pa msonkhano kamasangalatsa anthu otiona. Komabe, mmene timavalila nthawi zina monga pamene tifika pa mahotelo, pamene tikudya ku malesitilanti, popita kukagula zinthu kapena pocita zinthu zina, kangakhudze kwambili mmene anthu amationela. Nthawi zonse tiyenela kuvala zovala zoyenela komanso zaulemu ngakhale pamene sitili pa msonkhano. Anthu otiona ayenela kusiyanitsa pakati pa ife ndi anthu akunja. (Aroma 12:2) Kuonjezela apo, tiyenela kuvala mabaji athu a msonkhano, popeza zimenezi zidzacititsa kuti tikhale ndi mipata yolalikila, komanso kudzathandiza kuti opezeka pamsonkhano ena atizindikile.
3. Kodi tingaonetse bwanji kuleza mtima komanso ulemu?
3 Kuleza mtima ndi Ulemu: Panthawi ino, anthu ambili m’dzikoli ndi odzikonda kwambili komanso osayamika. Conco n’koyenela kuti tizikhala oleza mtima komanso aulemu kwa anthu ena maka-maka pamene tili ku hotelo ndi ku lesitilanti, cifukwa kucita zimenezi kudzawasangalatsa kwambili. (2 Tim. 3:1-5) Posunga malo okhala kapena poimilila pa mzela kuti titenge zofalitsa zimene zatulutsidwa pa msonkhano, tiyenela kuika zofuna za ena patsogolo m’malo mwa zofuna zathu. (1 Akor. 10:23, 24) Pambuyo pa kupezeka pa msonkhano wa cigawo kwa nthawi yoyamba, mwamuna wina anati: “Sindikumbukila nkhani iliyonse imene inapelekedwa tsiku lija, koma khalidwe la Mboni linandisangalatsa kwambili moti sindinaiŵale.”
4. N’cifukwa ciani tiyenela kuganiza zodzipeleka pa msonkhano ngati mikhalidwe yathu ilola?
4 Anchito Odzipeleka: Akristu oona amadziŵika cifukwa cokhala ofunitsitsa kudzipeleka. (Sal. 110:3) Kodi mungadzipeleke kuti muthandizeko pa msonkhano? Pamalo a msonkhano wina, abale ndi alongo okwana 600 anadzipeleka kuti adzayeletsa malo a msonkhano pulogalamu isanayambe. Eni malowo anati: “Ici ndi cinthu cosangalatsa kwambili cimene tikalibe kuonapo! Sitikhulupilila kuti anthu onsewa angodzipeleka.” Tikuyembekezela mwacidwi misonkhano ya cigawo ya 2013, komanso mwai umene tidzakhala nao womvetsela ndi kuphunzila kwa Mulungu komanso mwai waukulu womulemekeza.