◼ Nthawi ya Misonkhano: Anthu adzayamba kuloŵa pa malo a msonkhano ndi nthawi ya 07:00 hrs. Nyimbo zamalimba zidzayamba nthawi ya 08:20 hrs masiku onse atatu. Panthawi imeneyi, ife tonse tifunika kupeza malo okhalapo kuti msonkhano wathu udzayambe mwadongosolo ndi molemekezeka. Pa tsiku loyamba ndi laciŵili, nyimbo yomaliza ndi pemphelo lomaliza tizikhala nazo nthawi ya 15:55 hrs. Ndipo pa tsiku lacitatu ndi nthawi ya 15:10 hrs.
◼ Misonkhano ya Maiko: Malo ena kudzacitika misonkhano ya maiko. Dziŵani kuti ofesi ya nthambi yaitana mipingo yosankhidwa ndi alendo ocokela ku maiko ena, pambuyo poganizila malo okhala, malo oimikako magalimoto ndi malo ogona mu mahotelo. Ngati ofalitsa angapite ku msonkhano wa maiko umene sanaitanidwe, ndiye kuti kungakhale anthu oculuka kuposa amene afunika. Ngati mungalephele kupezeka pa msonkhano wanu wa cigawo ndiye mukufuna kukapezeka ku msonkhano wina, conde musadzasankhe kukapezeka pa msonkhano wa maiko. Mufunika kutsatila malangizo a akalinde amene akuyang’anila galimoto.
◼ Koimika magalimoto: Pa malo onse a msonkhano amene tapatsidwa mphamvu zoyang’anila malo oimikako magalimoto, malo azipatsidwa kwa munthu malinga ndi nthawi imene wafika. Nthawi zambili, malo oimikako magalimoto amacepa, conco ndi bwino kuyendela m’galimoto imodzi ngati zingatheke.
◼ Kusungilana Malo: M’mawa uliwonse, nthawi yoloŵa pa malo a msonkhano ikakwana, musacite kuthamanga kuti mukapeze malo amene mumawakonda monga ngati mukupikisana ndi anzanu. Mzimu wodzimana umene umatithandiza kucitila ena zabwino umaticititsa kudziŵika kuti ndife Akristu oona ndipo anthu otiona amalimbikitsidwa kutamanda Yehova. (Yoh. 13:34, 35; 1 Akor. 13:4, 5; 1 Pet. 2:12) Mungasungile malo anthu a m’banja lanu okha, kapena amene mwabwela nao m’galimoto imodzi kapenanso maphunzilo anu a Baibulo. Pakonzedwa malo okhala a odwala ndi okalamba. Popeza malo amenewa adzakhala ocepa, munthu mmodzi kapena aŵili ndi amene angakhale pamenepo kuti azisamalila odwala kapena okalamba.
◼ Cakudya ca Masana: Conde mukanyamuliletu cakudya ca masana kuti musadzacoke pa malo a msonkhano masana n’kupita kwina kukagula cakudya. Pa misonkhano imene idzacitikila m’bwalo la maseŵela lokhala ndi mipando, munganyamulile zakudya zanu m’nswanda kapena kuti basiketi imene ingakwane munsi mwa mpando wanu. Musadzabweletse zonyamulilamo zazikulu monga za ku pikiniki ndi zinthu za galasi pa malo a msonkhano amenewa.
◼ Zopeleka: Tingaonetse kuyamikila nchito imene inagwilidwa pokonzekela msonkhanowu popeleka mwaufulu ndalama zothandiza pa nchito ya padziko lonse, ndipo tingapeleke ndalamazi pamsonkhanopo. Polemba macheke opeleka pamsonkhano wa cigawo, sonyezani kuti ndalamazo zipita ku “Watch Tower Society.”
◼ Mankhwala: Ngati mumafunika mankhwala ocita kukulembelani ku cipatala, conde tsimikizilani kuti mukanyamule okwanila cifukwa ku msonkhano sadzakhalako. Masilenje ndi nyeleti zimene odwala matenda a shuga amagwilitsila nchito, siziyenela kutayidwa mu zinthu zotayilamo zinyalala pa malo a msonkhano, kapena pa hotelo. Zinthu zimenezi muyenela kuzisunga bwinobwino ndi kukazitaya mukapita kunyumba.
◼ Kupewa Ngozi: Conde, musakacititse ngozi iliyonse poika zinthu mwacisawawa zimene zingacititse ena kukhumudwa, kapena kukoledwa nazo ndi kugwa. Caka ciliconse anthu amadzipweteka cifukwa covala nsapato zazitali kwambili. Cingakhale bwino kuvala nsapato za ulemu, zokwana bwino zimene mudzakhoza kuyenda nazo bwinobwino pa malo alionse.
◼ Mapulemu ndi Mipando Yapanja: Mungabwele ndi zinthu zimenezi pa malo osankhidwa a misonkhano ya kumadela akumidzi ndi m’nyumba za misonkhano. Ngati msonkhano udzacitikila m’bwalo la maseŵela limene lili ndi mipando kale, simuyenela kubwela ndi mapulemu ndi mipando yapanja. Komabe, mungabwele ndi mipando yoikamo ana ngati idzaiikidwa pampando umene uli pafupi ndi makolo. Funsani akulu a mumpingo wanu za malangizo a kudela lanu.
◼ Mapefyumu: Kungakhale kuonetsa cikondi ngati tingasamale kwambili ndi kuculuka kapena mtundu wa pefyumu imene tingagwilitsile nchito. Izi zili conco cifukwa cakuti fungo lamphamvu la mapefyumu limacititsa anthu ena amene ali ndi matenda ovutika kupuma kuti adwale kwambili.—1 Akor. 10:24.
◼ Fomu ya Kaonaneni ndi Wacidwi Uyu (S-43): Fomu ya Kaonaneni ndi Wacidwi Uyu tingaigwilitsile nchito pofuna kudziŵikitsa munthu amene anaonetsa cidwi pa msonkhano pamene tinali kucita ulaliki wamwai. Tingapeleke mafomu amenewa ku Cipinda ca Mabuku kapena mungadzapatsile kalembela wa mpingo wanu mukadzabwelela ku nyumba.
◼ Utumiki Wodzifunila: Aliyense amene afuna kuthandiza nchito pa msonkhano wa cigawo, angalembetse ku Dipatimenti ya Anchito Odzifunila. Ana azaka 16 kubwela pansi, angagwile nchitoyi moyang’anilidwa ndi makolo ao kapena wacikulile aliyense amene kholo lingavomeleze.