Zikumbutso za Msonkhano wa Cigawo
Nthawi ya Misonkhano: Anthu adzayamba kuloŵa pa malo a msonkhano ndi nthawi ya 07:00hrs. Nyimbo zamalimba zidzayamba nthawi ya 08:20hrs masiku onse atatu. Panthawi imeneyi, ife tonse tifunika kupeza malo okhalapo kuti msonkhano wathu udzayambe mwadongosolo ndi molemekezeka. Pa tsiku loyamba ndi laciŵili, nyimbo ndi pemphelo lomaliza tizikhala nazo nthawi ya 15:50hrs. Ndipo pa tsiku lacitatu ndi nthawi ya 15:10 hrs.
‘‘Tamandani Yehova mwa Kuimba Nyimbo: M’nthawi yakale anthu a Yehova anali kum’tamanda mwa kuimba nyimbo. Masiku anonso, kuimba nyimbo ndi mbali yofunika polambila Yehova. (Sal. 28:7) Cigawo ciliconse ca msonkhano cimayamba ndi nyimbo zamalimba. Nyimbozi sizimakonzedwa ndi colinga congotisangalatsa cabe koma kuti tiphunzile za Yehova ndi kumulambila. Conco cheyamani wa msonkhano akalengeza kuti nyimbo zamalimba zakhala pang’ono kuyamba, tifunika kukhala pamalo athu ndi kumvetsela mwachelu m’malo molankhulana ndi ena. Kucita zimenezi kumasonyeza kuti tikuyamikila nchito imene abale oimba nyimbo anagwila. Kaŵili pa caka, abale ndi alongo amenewa, amagwilitsila nchito ndalama zao kupita ku Patterson, mu mzinda wa New York, n’colinga cokakonza nyimbo zotisangalatsa zimenezi. Pambuyo pomvetsela nyimbo zamalimba zimenezi, tonse tifunika kutamanda Yehova mwa kuimba nyimbo zathu za Ufumu.
Koimika Magalimoto: Pa malo onse a msonkhano amene tapatsidwa mphamvu zoyang’anila malo oimikako magalimoto, malo azipatsidwa kwa munthu malinga ndi nthawi imene wafika. Nthawi zambili, malo oimikako magalimoto amacepa, conco ndi bwino kuyendela m’galimoto imodzi ngati zingatheke. Tsatilani malangizo amene mungapatsidwe ndi abale oyang’anila magalimoto ndi njinga.
Kusungilana Malo: Tsiku lililonse polowa malo a msonkhano, musakacite kuthamanga kuti mukapeze malo okhala monga ngati mukupikisana ndi anzanu. Mzimu wodzimana umenewu umatilimbikitsa kucitila ena zabwino ndipo umatidziŵikitsa kuti ndife Akristu oona. Zimenezi zimalimbikitsa anthu otiona kutamanda Yehova. (Yoh. 13:34, 35; 1 Akor. 13:4, 5; 1 Pet. 2:12) Mungasungile malo anthu a m’banja lanu okha, kapena amene mwabwela nao m’galimoto imodzi kapenanso maphunzilo anu a Baibulo. Muziganizila ena pamene mukukhoma ma ambulela kapena kukonza malo okhala. Citani zinthu moganizila. Dzifunseni kuti: Kodi zimene tikucitazi zidzalephele ena kuona bwino ndi kupindula ndi mapulogalamu? Pakonzedwa malo okhala odwala ndi okalamba. Popeza malowa adzakhala ocepa, munthu mmodzi kapena aŵili ndi amene angakhale pamenepo kuti azisamalila odwala kapena okalamba.
Kuvala Moyenela: Pa msonkhano tiyenela kuvala moyenela ndi mwaulemu, osati motengela masitaelo ofala a ku dzikoli. (1 Tim. 2:9) Misonkhano isanayambe kapena ikatha tiyenela kupewa zovala zimene sizipatsa ulemu. Tikatelo tidzakhala onyadila kuvala baji ya msonkhano ndipo sitidzacita manyazi kulalikila ngati tapeza mpata. Maonekedwe athu ndi khalidwe lathu labwino tikadzapezeka pamisonkhano ikubwelayi, sizidzakopa cabe anthu a mtima wabwino kuyamba kuphunzila uthenga wa m’Baibulo wopulumutsa moyo koma zidzasangalatsanso Yehova.—Zef. 3:17.
Gwilitsilani Nchito Bwino Zipangizo Zina: Tingalemekeze pulogalamu yathu ya msonkhano mwa kusintha malilidwe a foni yathu kapena ya cipangizo cina kuti tisasokoneze ena. Mukhoza kujambula zithunzi pogwilitsila nchito kamela, zipangizo zojambulila vidiyo, matabuleti, ndi zina kucokela pamalo anu, koma citani zimenezo moganizila ena, kuti musawasokoneze kapena kuwacingiliza. Timasonyezanso ulemu ngati tipewa kutumilana mauthenga pulogalamu ili mkati.
Ubatizo: Malo aubatizo sayenela kukhala oseŵelelapo ana kapena kucita kulimbilana pojambula zithunzi. Onse amene adzapezekapo pa cocitika capadela cimeneci, adzafunika kuima capatali ndi kucita zinthu mwaulemu. Ngati padzapezeka ana, makolo ao kapena wina wacikulile ayenela kuwayang’anila.
Cakudya ca Masana: Conde mukanyamuliletu cakudya kuti musadzacoke pa malo a msonkhano n’kupita kwina kukagula cakudya. Munganyamulile zakudya zanu m’nswanda kapena kuti basiketi imene ingakwane munsi mwa mpando wanu. Zinthu za galasi pa malo a msonkhano si zololeka. Ndipo zakudya zotsala ndi zinyalalala zonse simuyenela kuzisiya pa malo a msonkhano.
Zopeleka: Tingaonetse kuyamikila nchito imene inagwilidwa pokonzekela msonkhanowu popeleka mwaufulu ndalama zothandiza pa nchito ya padziko lonse, ndipo tingapeleke ndalamazi pamsonkhanopo. Polemba macheke opeleka pamsonkhano wa cigawo, sonyezani kuti ndalamazo zipita ku “Watchtower Society.”
Mankhwala: Ngati mumafunika mankhwala ocita kukulembelani ku cipatala, conde tsimikizilani kuti mukanyamule okwanila cifukwa ku msonkhano sadzakhalako. Masilenje ndi nyeleti zimene odwala matenda a shuga amagwilitsila nchito, siziyenela kutayidwa mu zinthu zotayilamo zinyalala pa malo a msonkhano, kapena pa hotelo. Zinthu zimenezi muyenela kuzisunga bwinobwino ndi kukazitaya mukapita kunyumba.
Kupewa Ngozi: Conde, musakacititse ngozi iliyonse poika zinthu mwacisawawa zimene zingacititse ena kukhumudwa, kapena kukoledwa nazo ndi kugwa. Caka ciliconse anthu amadzipweteka cifukwa covala nsapato zazitali kwambili. Cingakhale bwino kuvala nsapato za ulemu, zokwana bwino zimene mudzakhoza kuyenda nazo bwinobwino pa malo alionse. Makolo ayenela kuonetsetsa kuti akuyang’anila bwino ana ao ndiponso kuti anawo asacititse ngozi. Ayenelanso kukhala okonzeka kupeleka malangizo ndiponso cilango kwa mwana wao ngati aona kuti zimene iye akucita zikusokoneza ena.
Mapulemu ndi Mipando Yapanja: Mapulemu ndi mipando yapanja ndi yololedwa cabe ku misonkhano yocitila panja. Komabe, mungabwele ndi mipando yoikamo ana ngati idzaiikidwa pampando umene uli pafupi ndi makolo.
Mapefyumu: Kungakhale kuonetsa cikondi ngati tingasamale kwambili ndi kuculuka kapena mtundu wa pefyumu imene tingagwilitsile nchito. Izi zili conco cifukwa cakuti fungo lamphamvu la mapefyumu limacititsa anthu ena amene ali ndi matenda ovutika kupuma kuti adwale kwambili.—1 Akor. 10:24.
Fomu ya Kaonaneni ndi Wacidwi Uyu (S-43): Fomuyi tingaigwilitsile nchito pofuna kudziŵikitsa munthu amene anaonetsa cidwi pa msonkhano pamene tinali kucita ulaliki wamwai. Tingapeleke mafomu amenewa ku Cipinda ca Mabuku kapena mungadzapatsile kalembela wa mpingo wanu mukadzabwelela ku nyumba.
Malesitilanti, Mashopu, ndi Malo Ena: Pamene muli ku malo amenewa muyenela kuonetsa khalidwe labwino limene lingalemekezetse dzina la Yehova. Muyenela kucita zinthu modekha ndi mwaulemu pamene mwakwela mabasi, muyendetsa galimoto kapena poyenda pa mseu. Valani zovala zoonetsa kuti ndinu mtumiki wa Mulungu.
Utumiki Wodzifunila: Aliyense amene afuna kuthandiza nchito pa msonkhano wa cigawo, angalembetse ku Dipatimenti ya Anchito Odzifunila. Ana azaka 16 kubwela pansi, angagwile nchitoyi moyang’anilidwa ndi makolo ao kapena wacikulile aliyense amene kholo lingavomeleze.