Abale Acinyamata, Kodi Mukukalamila?
1. Kodi m’bale wacinyamata angayambe liti kugwilitsila nchito mau opezeka pa 1 Timoteyo 3:1?
1 “Ngati munthu aliyense akuyesetsa . . . , akufuna nchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Mau awa ouzilidwa amalimbikitsa abale kukalamila maudindo mumpingo. Kodi muyenela kukhala wacikulile kuti mukalamile? Iyai, ndipo ndi bwino kukalamila pamene mukali wacinyamata. Mukatelo, mudzaphunzitsidwa ndipo nchito zanu zidzaonetsa kuti muli oyenelela kuikidwa kukhala mtumiki wothandiza mukasinkhukako. (1 Tim. 3:10) Ngati ndinu m’bale wacinyamata wobatizika, kodi mungakalamile bwanji?
2. Kodi mungakulitse ndi kuonetsa bwanji mzimu wa kudzipeleka?
2 Kudzipeleka: Kumbukilani kuti mukukalamila nchito yabwino, osati dzina. Conco, kulitsani cikhumbo cofuna kuthandiza abale ndi alongo anu. Njila imodzi yocitila zimenezi, ndiyo mwa kusinkha-sinkha citsanzo cabwino ca Yesu. (Mat. 20:28; Yoh. 4:6, 7; 13:4, 5) M’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kuti muzicita cidwi ndi ena. (1 Akor. 10:24) Kodi mungapelekeko cithandizo kwa anthu okalamba kapena olemala mumpingo? Kodi mumadzipeleka kuti mucheche kapena kuti mukhwape udzu, ndiponso kuti musamalile mbali zina zokonza Nyumba ya Ufumu? Kodi mumakonzekela kupeleka nkhani ya mwadzidzidzi m’Sukulu ya Ulaliki? Mukatelo, mudzapeza kuti kudzipeleka m’malo mwa ena kudzakupatsani cimwemwe.—Mac. 20:35.
3. Kodi kukhala wokhwima kuuzimu n’kofunika motani? Ndipo n’ciani cingathandize munthu kukhwima kuuzimu?
3 Kukhwima kuuzimu: Cinthu cofunika kwambili kwa mtumiki mu mpingo ndi kukhala wokhwima kuuzimu kuposa kukhala ndi maluso apadela. Munthu wa kuuzimu amayesa kuona zinthu monga mmene Yehova ndi Yesu amaonela. (1 Akor. 2:15, 16) Amaonetsa “makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Amakhala mlaliki wa cangu amene amaika Ufumu pamalo oyamba. (Mat. 6:33) Mungakhale ndi makhalidwe a kuuzimu mwa kukhala ndi cizoloŵezi cocita phunzilo laumwini. Zimenezi zingaphatikizepo, kuŵelenga Baibo tsiku lililonse, kuŵelenga magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani!, ndi kukonzekela misonkhano komanso kupezekapo. (Sal. 1:1, 2; Aheb. 10:24, 25) Polimbikitsa Timoteyo wacinyamata kuti apite patsogolo mwa kuuzimu, Paulo analemba kuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi zimene . . . Umaphunzitsa.” (1 Tim. 4:15, 16) Conco muzikonzekela bwino nkhani zanu za m’Sukulu ya Ulaliki. Muzikonzekela musanapite muulaliki, komanso muzicilikiza ulaliki nthawi zonse. Muzikhala ndi zolinga zanu za kuuzimu ndipo muzizikwanilitsa. Mwacitsanzo, mungakhale ndi zolinga monga, kucita upainiya, utumiki wa pa Beteli, kapena kupezeka ku Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Abale Osakwatila. Kukhala wokhwima kuuzimu kudzakuthandizani kuti ‘muthaŵe zilakolako zaunyamata.’—2 Tim. 2:22.
4. Kodi kukhala wodalilika ndi wokhulupilika n’kofunika motani?
4 Khalani Wodalilika Komanso Wokhulupilika: Popeza abale amene anapatsidwa nchito yogaŵa cakudya kwa Akristu ovutika m’zaka za zana loyamba anali “a mbili yabwino,” ndipo anali odziŵika monga abale odalilika komanso okhulupilika. Atumwi sanade nkhawa zakuti kaya ngati nchito idzacitika. Zimenezi zinapatsa atumwi mwai wakuti asamalile nkhani zina zofunika kwambili. (Mac. 6:1-4) Conco, mukapatsidwa nchito ndi mpingo, muyenela kuicita mmene mungathele. Tsanzilani Nowa, amene anatsatila mosamalitsa malangizo amene anapatsidwa kuti amange cingalawa. (Gen. 6:22) Kukhala wokhulupilika kumakondweletsa Yehova komanso kumaonetsa kukhwima kuuzimu.—1 Akor. 4:2; onani bokosi lakuti “Mapindu a Kuphunzitsidwa.”
5. N’cifukwa ciani abale acinyamata ayenela kukalamila?
5 Mogwilizana ndi ulosi, Yehova akufulumizitsa nchito yosonkhanitsa anthu. (Yes. 60:22) Pa avaleji, anthu pafupi-fupi 250,000 amabatizika caka ciliconse. Popeza atsopano ambili akubwela m’coonadi, pakufunika amuna oyenelela komanso okhwima kuuzimu kuti asamalile maudindo mumpingo. Kuposa kale lonse, pali nchito yambili yofunika kucita mu utumiki wa Yehova. (1 Akor. 15:58) Abale acinyamata, kodi mukukalamila? Ngati n’conco, ndiye kuti mukufuna nchito yabwino kwambili!
[Mau okopa papeji 2]
Popeza atsopano ambili akubwela m’coonadi, pakufunika amuna oyenelela komanso okhwima kuuzimu kuti asamalile maudindo mumpingo
[Bokosi papeji 3]
Mapindu a Kuphunzitsidwa
Abale acinyamata oyenelela amapindula pamene akulu awapatsa nchito ndi kuwaphunzitsa. Mwacitsanzo, woyang’anila dela anali pa pulatifomu akulimbikitsa wofalitsa wina pambuyo pamsonkhano. Ndiyeno anaona kamnyamata kena kanali ciimile capafupi, conco wadelayu anakafunsa ngati kanali kufuna kukamba naye. Kamnyamatako kanayankha kuti akulu anakauza kuti kaziyeletsa papulatifomu misonkhano iliyonse ikatha. Makolo ake anali okonzeka kupita, koma kamnyamataka sikanali kufuna kupita kasanacite nchito yake. Woyang’anila dela anasangalala kwambili. Ndipo anati: “Akulu mumpingowo anali kuphunzitsa abale acinyamata mwa kuwapatsa nchito mumpingo. Ndiye cifukwa cake nthawi zonse ndikamacezela mpingo wao anali kuyamikila abale acinyamata kuti ayenelele kutumikila monga atumiki othandiza.”