M’mwezi wa August Tidzakhala ndi Nchito Yapadela!
Tidzagaŵila Kapepala Kauthenga Katsopano Padziko Lonse
1. Kodi tidzakhala ndi nchito yapadela iti imene idzacitika padziko lonse pamene tikuyandikila zaka 100 za Ufumu?
1 Caka ca 100 kucokela pamene Ufumu wa Mulungu unabadwa cayandikila. Conco n’koyenela kuti tilemekeze Yehova mwa kucitako nchito yapadela. M’mwezi wa August tidzakhala ndi nchito yapadziko lonse yogaŵila kapepala kauthenga katsopano ka mutu wakuti: “Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?” Kapepalaka kakulimbikitsa anthu kupeza mayankho m’Baibulo ndipo kafotokozanso mmene jw.org ingawathandizile.
2. Kodi tingadzatengeko bwanji mbali pa ‘kufuula mokweza kwambili potamanda Yehova’ kumene kudzacitika mu August?
2 Kufuula Mokweza Kwambili Potamanda: Pofuna kuthandiza ofalitsa kuonjezela utumiki wao, makonzedwe apadela apangidwa akuti aliyense amene afuna angacite upainiya wothandiza m’mwezi wa August. M’mwezi umenewu, ofalitsa obatizika adzapatsidwa mwai wocita upainiya wothandiza wa maola 30. Popeza mwezi wa August udzakhala ndi masiku a Cisanu, Ciŵelu ndi Sondo asanu, ofalitsa ambili amene amagwila nchito mkati mwa mlungu adzatha kucita upainiya. Ngati muli ndi wophunzila Baibulo amene akwanilitsa ziyeneletso zokhala wofalitsa kapena mwana amene afuna kukhala wofalitsa, mwamsanga uzani mgwilizanitsi wa bungwe la akulu. Zidzakhaladi zolimbikitsa kwambili ngati anthu amenewa naonso angakhale ofalitsa m’mwezi wapadela umenewu. Ngakhale kuti apainiya okhazikika ambili pambuyo pokwanilitsa maola ao apacaka amakhala pachuti m’mwezi wa August umenewu, n’kutheka kuti angasinthe ndandanda yao ndi colinga cakuti atengeko mbali mokwanila m’nchito yapadela imeneyi. Ino ndiyo nthawi yabwino yakuti mabanja akambitsilane zimene angacite kuti adzatengeko mbali pa ‘kufuula mokweza kwambili potamanda Yehova’ kumene kudzacitika mu August.—Ezara 3:11; Miy. 15:22.
3. Kodi tili ndi ciyembekezo cotani ponena za nchito yapadelayi?
3 Ngakhale kuti m’mbuyomu tinacitako nchito yapadela yofanana, tikhulupilila kuti nchito imeneyi idzakhala yosaiŵalika. Kodi tingadzakhale ndi ziŵelengelo zapamwamba za maola, ofalitsa ndi apainiya othandiza mu August? Pamene tikumaliza caka cautumiki ca 2014, pemphelo lathu n’lakuti Yehova adalitse khama la anthu ake padziko lapansi kuti mwezi wa August udzakhale mwezi umene nchito yolalikila idzacitika kwambili kuposa miyezi yonse.—Mat. 24:14.