Sukulu ya Ulaliki ya 2015 Idzatithandiza Kunola Luso Lathu Lophunzitsa
1 Wamasalimo Davide analemba kuti: “Mau a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga, zikukondweletseni, inu Yehova, Thanthwe langa ndi Wondiombola.” (Sal. 19:14) Ifenso timafuna kuti mau athu azikondweletsa Yehova cifukwa timayamikila mwai wathu wolankhula za coonadi mumpingo ndiponso mu ulaliki. Sukulu ya Ulaliki ndi njila imodzi imene Yehova amatiphunzitsila kuti tizitha kulalikila. Sukulu imeneyi imacitika mlungu uliwonse m’mipingo yoposa 111,000 padziko lonse. Sukuluyi yathandiza abale ndi alongo osiyanasiyana padziko lonse kukhala atumiki oyenelela a uthenga wabwino, kuphunzitsa Baibulo mogwila mtima, mwaluso, komanso molimba mtima.—Mac. 19:8; Akol. 4:6.
2 Nkhani zina zimene zidzakhala m’ndandanda ya sukulu ya 2015 zidzatengedwa m’buku lakuti “Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu”[sgd-CIN], “Mfundo za mu Mau a Mulungu” [igw-CIN], Nsanja ya Mlonda kapena Nsanja ya Olonda, ndiponso “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu” [lv-CIN]. Kuonjezela pamenepo, nthawi yokamba mfundo zazikulu ndiponso Nkhani Na.1 yacepetsedwa. Ndime zotsatilazi zifotokoza ponena za masinthidwe amenewa ndiponso mmene nkhani za m’sukuluyi ziyenela kukambidwa.
3 Mfundo Zazikulu: Abale amene adzapatsidwa nkhaniyi ayenela kufotokoza mfundo imodzi yolimbikitsa ndi yothandiza ya m’Malemba kwa mphindi ziŵili yocokela m’kuŵelenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu. Kukonzekela bwino kudzathandiza kuti abalewo afotokoze mfundo yolimbikitsa popanda kudya nthawi. Ndiyeno, mpingo udzapatsidwa mphindi 6, ndipo m’bale kapena mlongo aliyense ayenela kufotokoza kwa masekondi 30 mfundo imene anapindula nayo pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu. Kukonzekela bwino n’kofunika kuti muyesetse kufotokoza mfundo yothandiza kwa masekondi 30, ndipo kucita zimenezo kudzatipindulitsa. Kudzapatsanso ena nthawi yokambapo pa zimene anaphunzila pa kuŵelenga Baibulo.
4 Nkhani Na. 1: Mbali ya kuŵelenga Baibulo izicitika kwa mphindi zitatu kapena zocepelapo ndipo izikhala ndi mfundo zocepa. Abale amene adzapatsidwa nkhani yoŵelenga ayenela kuyeseza kangapo mwa kuŵelenga mokweza. Ayenela kuzindikila kachulidwe kabwino ka mau kuti amveketse bwino ciganizo. Atumiki onse a Yehova ayenela kuyesetsa kuŵelenga bwino cifukwa kuŵelenga ndi mbali yofunika kwambili pa kulambila kwathu. Ndife okondwa kwambili kuti ana athu ambili amaŵelenga bwino. Ndipo tikuyamikilani inu makolo cifukwa ca khama lanu pothandiza ana anu kuti akhale aŵelengi abwino.
5 Nkhani Na. 2: Iyi ndi nkhani ya alongo ya mphindi zisanu. Afunikila kugwilitsila nchito mutu wa nkhani imene apatsidwa. Ngati nkhani yacokela mu Buku Lothandiza pophunzila Baibulo kapena kabuku kakuti Mfundo za m’Mau a Mulungu, wophunzila ayenela kugwilizanitsa nkhaniyo ndi zocitika za mu ulaliki m’gawo la mpingo wao. Ngati nkhaniyo ikufotokoza za munthu winawake wa m’Baibulo amene wachulidwa mu Nsanja ya Mlonda kapena Nsanja ya Olonda, wophunzila ayenela kuŵelenga za munthu wochulidwa m’Baibulo, kusankha malemba oyenelela, ndi kufotokoza zimene tikuphunzilapo kwa munthuyo. Angagwilitsilenso nchito malemba ena amene akugwilizana ndi mutu wa nkhani. Woyang’anila sukulu adzasankha munthu mmodzi kuti akhale wothandizila.
6 Nkhani Na. 3: Iyi ndi nkhani ya mphindi zisanu imene ingapatsidwe kwa m’bale kapena mlongo. Mlongo akapatsidwa nkhani imeneyi, aziikamba mofanana ndi nkhani Na. 2. Nkhani ikacokela mu Nsanja ya Mlonda, kapena m’buku lakuti “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu,” izikhala nkhani yokambila omvela. Wophunzila ayenela kumveketsa mutu wankhaniyo, kusankha malemba oyenelela ogwilizana ndi nkhaniyo, ndi kufotokoza zimene tingaphunzilepo pa citsanzo ca munthu winawake wochulidwa m’Baibulo.
7 Mbali Yatsopano Yokhudza Nkhani Na. 3 ya Abale: Ngati nkhaniyi yacokela mu Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu, kapena kabuku kakuti Mfundo za m’Mau a Mulungu iyenela kupelekedwa monga mucita kulambila kwa pabanja kapena utumiki wakumunda. Nthawi zambili, woyang’anila sukulu azikugaŵilani wokuthandizani ndiponso makambilano. Wothandizayo ayenela kukhala wam’banja la wophunzilayo kapena m’bale wa mumpingo. Pokamba nkhaniyo mungaphatikizepo Malemba ena amene afotokoza mfundo za m’Baibulo zogwilizana ndi mutu wa nkhani. Nthawi ndi nthawi mkulu angapatsidwe kukamba nkhani imeneyi. Akulu angasankhe okha makambilano ndiponso owathandiza. Mwacionekele, mpingo udzalimbikitsidwa kwambili kuona akulu akuonetsa luso lao lophunzitsa ali ndi wapabanja lao kapena m’bale wina.
Pitani patsogolo mwa kulandila uphungu ndi kuugwilitsila nchito
8 Uphungu: Woyang’anila sukulu azigwilitsila nchito mphindi ziwili poyamikila kapena popeleka uphungu wothandiza kwa wophunzila amene wakamba nkhani. Uphungu umenewu uyenela kucokela m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Pamene woyang’anila sukulu aitanila mbali ya wophunzila, sadzafunikila kuchula mfundo imene wophunzilayo akugwililapo nchito. Koma wophunzila akamaliza kukamba nkhani, woyang’anila sukulu ayenela kumuyamikila mocokela pansi pamtima, kuchula mfundo imene wophunzilayo akugwililapo nchito, ndiponso cifukwa cake wophunzilayo wacita bwino pa mfundo imeneyo. Muyenela kufotokoza mokoma mtima cifukwa cake zingakhale zothandiza ngati wophunzilayo angagwilileponso nchito pa mfundoyo.
9 Fomu yolangizila ya wophunzila ipezeka pa tsamba 79 mpaka 81 m’buku lake la Pindulani. Wophunzila akakamba nkhani yake, woyang’anila sukulu azilemba mfundo zoyenelela m’buku la wophunzilayo ndipo mwamseli azifunsa wophunzila ngati anasamalila mbali ya zocita yogwilizana ndi mfundo imene anali kugwililapo nchito. Pambuyo pa misonkhano kapena nthawi ina, mungayamikile wophunzila ndi kumupatsa malangizo ena othandiza. Malangizo amene wophunzila aliyense amalandila m’sukulu ayenela kuwaona kukhala mwai womuthandiza kupita patsogolo mwa kuuzimu.—1 Tim. 4:15.
10 Wophunzila akadya nthawi, woyang’anila sukulu kapena wothandiza wake ayenela kupeleka cizindikilo monga kuliza belu kapena kumenya penapake, kuti aonetse mocenjela kuti nthawi ya wophunzila yatha. Wophunzila ayenela kulabadila cizindikiloco mwakumaliza ciganizo cimene akukambaco ndi kucoka pa pulatifomu.—Onani buku la Pindulani, tsa. 282, ndime 4.
11 Onse amene amakwanilitsa ziyeneletso akulimbikitsidwa kulembetsa m’Sukulu ya Ulaliki. (Onani buku la Pindulani, tsa. 282, ndime 6.) Maphunzilo amene sukulu imeneyi imapeleka athandiza anthu a Yehova kulalikila ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu mwacidalilo, mwaulemu ndi mwacikondi. Mosakaikila, Yehova amasangalala kwambili kutamandidwa ndi anthu onse amene akupindula kwambili ndi maphunzilo aumulungu.—Sal. 148:12, 13; Yes. 50:4.