Gaŵanani ndi Ena “Zabwino” mwa Kukhala Woceleza (Mat. 12:35a)
Mwacionekele tonse timafuna kugaŵana ndi ena zinthu “zabwino” mwa kukhala “oceleza.” (Aroma 12:13) Akulu amalangizidwa kuti afunika kupeleka citsanzo cabwino pa nkhani imeneyi mwa kupeleka ndalama zoyendela kwa abale odzakamba nkhani mumpingo mwao ndiponso kuwapatsa cakudya. Komabe, mwina tingalephele kusonyeza mzimu woceleza cifukwa cakuti ndife osauka, kapena cifukwa cocita manyazi kuitanila alendo ku nyumba kwathu. Kukumbukila malangizo amene Yesu anauza Malita kungatithandize kuthetsa maganizo amenewa. (Luka 10:39-42) Yesu ananena kuti “cinthu cabwino kwambili” pa kuceleza ena ndi mayanjano abwino ndi olimbikitsa osati cakudya capamwamba kapena nyumba yokongola. Ngati titsatila malangizo amenewa, tonse tingagaŵane ndi abale athu zinthu “zabwino” mogwilizana ndi zimene Mau a Mulungu amanena.—3 Yoh. 5-8.