“Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kupeza Anthu Owapelekela Magazini”
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Anthu ambili amene amakonda kuŵelenga magazini athu safuna kuphunzila nafe Baibulo. Ena amakana cifukwa cokonda kwambili cipembezo cao, kapena amaona kuti alibe nthawi yophunzila. Komabe, pamene akuŵelenga magazini athu nthawi zonse, angayambe kulakalaka kuphunzila Mau a Mulungu. (1 Pet. 2:2) Nkhani inayake ya m’magazini ingawakhudze kwambili, kapena zocitika pa umoyo wao zingasinthe. Tikamawacezela mwacidule nthawi zonse, angayambe kumasuka nafe ndipo tingadziŵe zokonda zao ndi zimene zimawadetsa nkhawa. M’kupita kwa nthawi tingayambe kuphunzila nao Baibulo.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Lembani maina a anthu amene afuna kuti muziwapelekela magazini. Apatseni magazini atsopano ndi kuwauza kuti mudzawabweletsela ena mwezi wotsatila.