Phunzilani kwa Ofalitsa Amene Atumikila Zaka Zambili
Timayamikila kwambili kukhala ndi ofalitsa amene atumikila zaka zambili mumpingo. Ena mwa io aphunzila maluso a mu ulaliki posacedwapa ndipo ena atumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili. Ofalitsawa aona mmene Yesu akutsogolela mpingo wacikristu m’masiku otsiliza ano mwa kufutukula nchito yolalikila ndi kupanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20) Pogwila nchito imeneyi, ofalitsawa amakumana ndi mavuto ndi ziyeso zosiyanasiyana, koma Mulungu amawapatsa “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti apilile. (2 Akor. 4:7) Tingaphunzile zambili kwa ofalitsa amene atumikila zaka zambili amenewa. Akapatsidwa mwai, amasangalala kuuzako ena zimene aphunzila. (Sal. 71:18) Conco tiyenela kupatula nthawi yophunzila kwa io. Koma kodi tingacite bwanji zimenezo?
Mu Ulaliki: Ofalitsa atsopano kapena ofalitsa amene ali ndi cidziŵitso cocepa afunika kuphunzitsidwa kuti azilalikila mogwila mtima. Conco angaphunzile zambili akamaona mmene ofalitsa ozoloŵela amacitila mu ulaliki. (Onani nkhani ya mutu wakuti: “Pitilizani Kukhala Wacangu mu Utumiki,” mu Nsanja ya Mlonda ya February 15, 2015 ndime 3 pa kamutu kakuti “Thandizani Atsopano.”) Kodi mwapindula bwanji polalikila ndi ofalitsa ozoloŵela amenewa?
Mungapemphe wofalitsa waluso kuti mugwile naye nchito yolalikila. Ngati wofalitsayo ndi wodwala, mungakaphunzilile Baibulo kunyumba kwake ndi munthu amene mumaphunzila naye Baibulo. Mukamaliza kuphunzila, mungamupemphe kuti akuuzeni mmene waonela phunzilolo ndi zimene mungaongolele.
Kuceza Nao: Muzipatula nthawi yoceza ndi ofalitsa aluso n’colinga cakuti muwadziŵe bwino. Pemphani mmodzi wa ofalitsawo kuti adzakhalepo pa kulambila kwanu kwa pa banja ndi kumupempha kuti akuthandizeni. Ngati wofalitsayo ndi wodwala, kodi mungakonze zokacitila kunyumba kwake kulambila kwanu kwa pabanja? Mungamufunse mmene anaphunzilila coonadi, madalitso amene wapeza, kusintha kumene waona m’delalo ndiponso cimene cimamusangalatsa kwambili potumikila Yehova.
Komabe sitiyenela kuyembekezela zimene sangakwanitse, m’malo mwake tiyenela kuwamvetsetsa. Iwo mofanana ndi wina aliyense ali ndi mphatso zosiyanasiyana. (Aroma 12:6-8) Ena angakhale acikulile, ndipo zimenezi zingacititse kuti aceze nafe nthawi yocepa. Ngakhale n’telo, tingaphunzile zambili kwa io cifukwa atumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili.