UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Aphunzitseni Kutumikila Yehova Mosalekeza
Maumboni aonetsa kuti ofalitsa acatsopano akaphunzitsidwa kulalikila nthawi zonse, ndiponso mwacangu kucokela paciyambi, amadzakhala ofalitsa ocita bwino. (Miy. 22:6; Afil. 3:16) Munsimu muli malingalilo amene angakuthandizeni kuphunzitsa wophunzila wanu kukhala na ciyambi cabwino cokonda ulaliki:
Wophunzila wanu akangovomelezedwa kukhala wofalitsa, yambani kum’phunzitsa. (km 8/15 peji 1) M’thandizeni kuona kufunika kophatikiza ulaliki pa pulogilamu yake ya wiki iliyonse. (Afil. 1:10) Muzikamba zabwino zokhudza gawo lolalikilamo. (Afil. 4:8) M’limbikitseni kulalikilako na woyang’anila kagulu, na ofalitsa ena kuti atengeko maluso.—Miy. 1:5; km 10/12 peji 6 pala. 3
Wophunzila wanu akabatizika, musaleke kum’limbikitsa na kum’phunzitsa ulaliki, maka-maka ngati sanatsilize kuphunzila buku lakuti “Khalanibe m’Cikondi.”—km 12/13 peji 7
Polalikila na wofalitsa watsopano, muziseŵenzetsa ulaliki wosavuta. Pambuyo poona ulaliki wake, muyamikileni mocokela pansi pamtima. Pelekani malingalilo omuthandiza kukhala wofalitsa waluso.—km 5/10 peji 7