Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Phunzitsani Atsopano
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Ophunzila a Yesu atsopano afunika kuphunzila ndi kusunga “zinthu zonse” zimene Yesu analamulila, kuphatikizapo kuphunzitsa ena coonadi. (Mat. 28:19, 20) Atsopano ambili avomelezedwa kuloŵa Sukulu ya Ulaliki ndipo mwina amacita ulaliki wamwai kwa a m’banja lao kapena kwa anzao. Iwo akamvetsetsa zimene akuphunzila ndi kuzindikila kuti Yehova afuna kuti anthu onse amve uthenga wabwino, amafunitsitsa kulalikila. (Aroma 10:13, 14) Atsopano akavomelezedwa kukhala ofalitsa osabatizidwa, afunika kuphunzitsidwa kuti asamadzikayikile pamene akuyesetsa kukula mwa kuuzimu.—Luka 6:40.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Pitani ndi wophunzila Baibulo wanu amene ndi wofalitsa watsopano mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, kuulendo wobwelelako kapena ku phunzilo la Baibulo. Ngati mulibe phunzilo la Baibulo limene ndi wofalitsa watsopano, mungapemphe ofalitsa amene sanazoloŵele kugwila nchito yolalikila.