CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ine Ndilipo! Nditumizeni.”
Mzimu wodzipeleka wa Yesaya, tiyeneladi kuutengela. Iye anaonetsa cikhulupililo mwa kuyankha mwamsanga pempho olo kuti sanali kudziŵa zoloŵetsedwamo. (Yes. 6:8) Kodi na imwe mungasintheko zinthu zina mu umoyo wanu kuti mukatumikileko kumene ofalitsa Ufumu ni ocepa? (Sal. 110:3) Cofunika, ni kuŵelengela mtengo mukalibe kusamuka. (Luka 14:27, 28) Komanso, khalani na mtima wodzimana kuti nchito yolalikila ipite patsogolo. (Mat. 8:20; Maliko 10:28-30) Monga taonela mu vidiyo yakuti Kukatumikila ku Malo Osoŵa, madalitso amene timalandila mu utumiki wa Yehova sitingawayelekezele na zinthu zimene timadzimana.
MUKATAMBA VIDIYO, YANKHANI MAFUNSO AYA:
Kodi a m’banja la William anadzimana zinthu zanji kuti akatumikile ku Ecuador?
Ni zinthu ziti zimene anaganizilapo posankha kumene angakatumikile?
Ni madalitso anji amene anapeza?
Ngati mufuna kudziŵa zambili pankhani yokatumikila kosoŵa, ni kuti kumene mungapeze malangizo?
PA KULAMBILA KWANU KWA PABANJA KOTSATILA, MUKAKAMBILANE MAFUNSO AYA:
Kodi tingawonjezele bwanji utumiki wathu monga banja? (km 8/11 4-6)
Ngati sitingakwanitse kukatumikila kosoŵa, tingathandize mpingo wathu m’njila ziti? (w16.03 tsa. 23-25)