UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kulitsani Makhalidwe Aumulungu—Kulimba Mtima
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA:
Kulalikila kumafuna kulimba mtima. —Mac. 5:27-29, 41, 42
Cisautso cacikulu cidzatiyesa pa kulimba mtima kwathu.—Mat. 24:15-21
Kuopa anthu kumabweletsa mavuto. —Yer. 38:17-20; 39:4-7
MMENE TINGAKULITSILE KULIMBA MTIMA:
Sinkha-sinkhani za mmene Yehova anapulumutsila anthu.—Eks. 14:13
Pemphani Mulungu kuti mukhale olimba mtima.—Mac. 4:29, 31
Dalilani Yehova.—Sal. 118:6
Ni mantha a ciani mu utumiki wanga amene niyenela kugonjetsa?
TAMBANI VIDIYO YAKUTI MUZIPEWA ZINTHU ZIMENE ZINGAKULEPHELETSENI KUKHALA WOKHULUPILIKA —KUOPA ANTHU, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
N’cifukwa ninji kulimba mtima n’kofunika mu utumiki?
Kodi pa Miyambo 29:25 pali zinthu ziŵili ziti zosiyana?
N’cifukwa ciani tifunika kukulitsa khalidwe la kulimba mtima pali pano?