UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Cilimikani Pamene Mapeto Ayandikila
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Posacedwa, zocitika zocititsa mantha zidzatiika pa mayeso pankhani ya kulimba mtima kwathu na cidalilo cathu mwa Yehova kuposa kale lonse. Cisautso cacikulu cidzayamba na kuwonongedwa kwa cipembedzo conyenga. (Mat. 24:21; Chiv. 17:16, 17) Pa nthawi ya zocitika zimenezi, mwina tidzayamba kulalikila uthenga waciweluzo woŵaŵa. (Chiv. 16:21) Tidzaukilidwa na Gogi wa Magogi. (Ezek. 38:10-12, 14-16) Pofuna kuteteza anthu ake, Yehova adzabweletsa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ (Chiv. 16:14, 16) Kuti tikhale olimba mtima kwambili poyembekezela zocitika za kutsogolo zimenezi, tifunika kukhala wokhulupilika pamene cikhulupililo cathu ciyesedwa pali pano.
MMENE TINGACITILE:
Molimba mtima sungani miyezo yapamwamba ya Yehova.—Yes. 5:20
Pitilizani kulambila pamodzi na Akhristu anzanu.—Aheb. 10:24, 25
Khalani okonzeka kumvela malangizo ocokela ku gulu la Yehova.—Aheb. 13:17
Sinkha-sinkhani mmene Yehova anapulumutsila anthu ake m’nthawi yakumbuyo.—2 Pet. 2:9
Pemphelani kwa Yehova, ndiponso mudalileni.—Sal. 112:7, 8
TAMBANI VIDIYO YAKUTI ZOCITIKA ZAM’TSOGOLO ZIMENE ZIDZAFUNA KULIMBA MTIMA—KAMBALI KAKE, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi ofalitsa anakumana na ciyeso cotani pankhani yakumvela pamene mpingo wawo unaphatikizidwa kumipingo ina?
Kodi kulimba mtima na kumvela zigwilizana bwanji?
N’cifukwa ciani kulimba mtima n’kofunika pamene Aramagedo ibwela?
Konzekelani pali pano zocitika za kutsogolo zimene zidzafuna kulimba mtima
Ni nkhani iti m’Baibo imene ingatithandize kulimbitsa cikhulupililo cathu cakuti Yehova adzakwanitsa kutipulumutsa?—2 Mbiri 20:1-24