Agaŵila kapepa kauthenga kakuti Akufa Angakhalenso Ndi Moyo m’Cituvalu
Maulaliki a Citsanzo
GALAMUKANI!
Funso: N’cifukwa ciani tifunika kukonzekela masoka a zacilengedwe?
Lemba: Miy. 27:12
Cogaŵila: Galamukani! iyi ifotokoza zimene tingacite masoka akalibe kucitika, panthawi ya masoka, na pambuyo pake?
PHUNZITSANI COONADI
Funso: Kodi tingaonetse bwanji kuti timam’konda Mulungu?
Lemba: 1 Yoh. 5:3
Coonadi: Timaonetsa cikondi cathu kwa Mulungu mwa kumvela malamulo ake.
KODI N’ZOONA KUTI AKUFA ANGAKHALENSO NDI MOYO? (T-35)
Funso: Anthu ambili oona mtima padziko lapansi amacita miyambo yokumbukila akufa. Kodi pali ciyembekezo cakuti tidzaonananso na okondedwa athu amene anamwalila?
Lemba: Mac. 24:15
Cogaŵila: Kapepa kauthenga aka kafotokoza mapindu okhulupilila kuti akufa adzauka. [Ngati n’kotheka, m’tambitseni kavidiyo kakuti Kodi Pali Ciyembekezo Cakuti Akufa Adzauka?]
KONZANI ULALIKI WANU
Funso:
Lemba:
Cogaŵila: