CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 13-14
Pewani Msampha wa Kuopa Anthu
N’cifukwa ciani atumwi anathaŵa zinthu zitavuta?
Anadzidalila kwambili. Ndipo Petulo anafika podziona kuti adzakhulupilika ngako kwa Yesu kuposa atumwi ena onse
Analephela kukhalabe maso na kupemphela
Yesu ataukitsidwa, n’ciani cinathandiza atumwi kupewa msampha wa kuopa anthu na kupitiliza kulalikila olo kuti anali kutsutsidwa?
Anamvela macenjezo a Yesu, ndipo anali okonzeka kupilila citsutso na cizunzo
Anadalila Yehova mwa kupemphela.—Mac. 4:24, 29
N’zocitika ziti zimene zingafune kuti tikhale olimba mtima?