CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 13-14
“Ndakupatsani Citsanzo”
Mwa kusambika mapazi a atumwi ake, Yesu anawaphunzitsa kuti afunika kukhala odzicepetsa komanso okonzeka kugwila nchito zotsika potumikila ena.
Ningaonetse bwanji kuti ndine wodzicepetsa pamene . . .
tayambana kapena kusemphana maganizo na wina?
wina akunilangiza kapena kunipatsa uphungu?
alengeza kuti kuli kuyeletsa na kukonza zinthu pa Nyumba ya Ufumu?