CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 13-14
“Cilimikani ndi Kuona Cipulumutso ca Yehova”
14:13, 14, 21, 22, 26-28
Yehova ni mpulumutsi amene amaganizila ena. Kodi anaonetsa bwanji kuwaganizila Aisiraeli pamene anali kutuluka mu Iguputo?
Anawayendetsa mwadongosolo.—Eks. 13:18
Anawatsogolela na kuwateteza.—Eks. 14:19, 20
Anapulumutsa anthu ake onse, kuyambila ana mpaka okalamba.—Eks. 14:29, 30
Kodi mungakhale otsimikiza za ciani pamene cisautso cacikulu cikuyandikila?—Yes. 30:15