CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 12
Mwambo wa Pasika—Zimene Umatanthauza kwa Akhristu
12:5-7, 12, 13, 24-27
Kuti Aisiraeli apewe kuvulazidwa na mlili wa namba 10, iwo anafunika kumvela malangizo. (Eks. 12:28) Usiku, pa Nisani 14, mabanja anasonkhana pamodzi m’nyumba zawo. Iwo anafunika kupha nkhosa kapena mbuzi yopanda cilema, yamphongo, ya caka cimodzi. Magazi ake anafunika kuwawaza pa mafelemu a nyumba zawo, komanso pamwamba pa khomo. Ndiyeno anafunika kuwocha nyama yonse na kuidya mofulumila. Munthu aliyense sanafunike kutuluka m’nyumba yake mpaka m’mawa.—Eks. 12:9-11, 22
Kodi kumvela kumatiteteza m’njila zina ziti masiku ano?