UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Tsatilani Mapazi a Khristu Mosamala Kwambili
Yesu anapeleka citsanzo cimene tiyenela kutengela, maka-maka ngati tikuyesedwa kapena kuzunzidwa. (1 Pet. 2:21-23) Olo kuti Yesu ananyozedwa na kuvutitsidwa, iye sanabwezele. (Maliko 15:29-32) N’ciani cinamuthandiza kupilila? Anali wofunitsitsa kucita cifunilo ca Yehova. (Yoh. 6:38) Cina, anasumika maganizo ake pa “cimwemwe cimene [Mulungu] anamuikila patsogolo pake.”—Aheb. 12:2.
Kodi timacita ciani ngati tivutitsidwa cifukwa ca cikhulupililo cathu? Akhristu oona ‘sabwezela coipa pa coipa.’ (Aroma 12:14, 17) Ngati titengela citsanzo ca Khristu ca kupilila, tidzakhala acimwemwe podziŵa kuti Mulungu akutiyanja.—Mat. 5:10-12; 1 Pet. 4:12-14.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI DZINA LA YEHOVA N’LOFUNIKA KWAMBILI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
Pamene Mlongo Pötzingera anali m’ndende ya yekha, kodi anaiseŵenzetsa bwanji nthawi mwanzelu?
Ni mavuto anji amene M’bale na Mlongo Pötzinger anapilila pamene anali m’ndende za cibalo?
N’ciani cinawathandiza kupilila?
Mukamavutika, muzitsatila mapazi a Khristu mosamala kwambili
a Dzinali amailembanso kuti Poetzinger.