UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kondwelani Pamene Mukuzunzidwa
Akhristu amadziŵa kuti adzazunzidwa. (Yoh. 15:20) Ngakhale kuti cizunzo cimabweletsa nkhawa komanso cimakhala cowawa, timakhala acimwemwe tikapilila.—Mat. 5:10-12; 1 Pet. 2:19, 20.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI TINGAKHALEBE OKONDWELA NGAKHALE PA MAZUNZO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi mwaphunzila ciyani kwa M’bale Bazhenov pa nkhani ya
kufunika koŵelenga Baibo tsiku lililonse?
kulandila thandizo locokela kwa Akhristu anzanu?a
kupemphela nthawi zonse?
kuimba nyimbo za Ufumu?
kuuzako ena za cikhulupililo canu?
a Tingapemphelele abale amene ali m’ndende, ngakhale kuchula maina awo. Komabe, n’zosatheka kuti ofesi ya nthambi ilembele kalata aliyense wa iwo.