UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Webusaiti Yathu ya JW.ORG
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Cofalitsa ciliconse cophunzitsila Baibo ca mu Thuboksi yathu, cimatsogolela anthu ku webusaiti yathu ya jw.org. Ndipo tumakhadi tongenela pa webusaiti komanso kapepa kakuti Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo? colinga cake cacikulu ni kutsogolela anthu ku webusaiti yathu. Mungaseŵenzetse webusaiti ya jw.org pogaŵila cofalitsa cophunzitsila Baibo ca mu Thuboksi yathu. Mungacite zimenezi mwa kutumizila munthu cofalitsaco pa imelo kapena mwa kumutumizila linki. Kucita izi kungakhale kothandiza kwambili maka-maka polalikila munthu amene amakamba citundu cina. Kuwonjezela apo, anthu angatifunse mafunso amene mayankho ake sapezeka m’zofalitsa za mu Thuboksi yathu. Zikakhala conco, tingaseŵenzetse webusaiti yathu, ndipo ulaliki wathu ungakhale wogwila mtima.
MMENE TINGACITILE:
Seŵenzetsani mbali yakuti “ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA” (imene ipezeka ku Chichewa). Ngati mukulalikila kholo, ndipo lifuna kudziŵa zambili zokhudza kulela ana, mungapite pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU OKWATIRANA KOMANSO MABANJA.
Seŵenzetsani mbali yakuti “MABUKU.” Ngati mukucita ulaliki wamwayi ku sukulu, ndipo mufuna kugaŵila mnzanu wa m’kalasi kabuku kakuti Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa, mungapite pa MABUKU > MABUKU NDI TUMABUKU.
Seŵenzetsani mbali yakuti “ZOKHUDZA IFE.” Ngati mukulalikila mnzanu wa ku nchito amene afuna kuŵelengako zimene ise timakhulupilila, mungapite pa ZOKHUDZA IFE > MAFUNSO OFUNSIDWA KAŴILIKAŴILI OKHUDZA MBONI ZA YEHOVA.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI KUSEŴENZETSA WEBUSAITI YATHU YA JW.ORG, NDIYENO GANIZILANI KUMENE MUNGAPITE PA WEBUSAITI YATHU KUTI MUTHANDIZE:
munthu amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu
munthu amene wakumana na tsoka
m’bale kapena mlongo wozilala
munthu amene munamulalikila, ndipo afuna kudziŵa mmene timapezela ndalama zoyendetsela nchito yathu
munthu wa ku dziko lina amene afuna kukapezeka pa misonkhano m’dziko lawo