UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Onetsani Khalidwe la Kudzicepetsa Monga Khristu
Ngakhale kuti Yesu anali wamkulu kuposa munthu aliyense amene anakhalako, anaonetsa kudzicepetsa mwa kulemekeza Yehova. (Yoh. 7:16-18) Mosiyana na Yesu, Satana anakhala Mdyelekezi, dzina lotanthauza “Woneneza.” (Yoh. 8:44) Khalidwe la Satana linaonekela mwa Afarisi, amene kunyada kwawo kunawapangitsa kusuliza munthu aliyense wokhulupilila mwa Mesiya. (Yoh. 7:45-49) Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pamene tapatsidwa udindo mu mpingo?
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—PEWANI NSANJE NDI KUDZITAMA, MBALI 1, PAMBUYO PAKE, KAMBILANANI ZOTSATILAZI:
Kodi Alex anaonetsa bwanji kunyada?
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—PEWANI NSANJE NDI KUDZITAMA, MBALI 2, PAMBUYO PAKE, KAMBILANANI ZOTSATILAZI:
Kodi Alex anaonetsa bwanji kudzicepetsa?
Kodi Alex analimbikitsa bwanji Bill na Carl?
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—PEWANI KUNYADA NDI KUCITA ZOSAYENELA, MBALI 1, PAMBUYO PAKE, KAMBILANANI ZOTSATILAZI:
Kodi M’bale Harris analephela bwanji kuonetsa khalidwe la kudzicepetsa?
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—PEWANI KUNYADA NDI KUCITA ZOSAYENELA, MBALI 2, PAMBUYO PAKE, KAMBILANANI ZOTSATILAZI:
Kodi M’bale Harris anaonetsa bwanji khalidwe la kudzicepetsa?
Kodi citsanzo ca M’bale Harris cinam’phunzitsa ciani Faye?