UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mapindu a pa Dziko Lonse a Ulaliki wa pa Kasitandi
Kulingana na Machitidwe caputa 5, Akhristu a m’nthawi ya atumwi anapita ku kacisi, malo amene kunali kupezeka anthu ambili kuti akalalikile uthenga wabwino. (Mac. 5:19-21, 42) Masiku ano, taona zotulukapo zabwino za ulaliki wapoyela wa tumasitandi.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MAPINDU A ULALIKI WA KASITANDI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
Kodi ulaliki wa pa kasitandi unayamba liti? Nanga unayamba bwanji?
Kodi kuseŵenzetsa kasitandi kuli na ubwino wanji kuposa kuseŵenzetsa thebulo?
Kodi cocitika ca mlongo Mi Jung You citiphunzitsa ciani?
Kodi cocitika ca m’bale Jacob Salomé cionetsa bwanji kufunika kwa ulaliki wa pa kasitandi?
Kodi cocitika ca mlongo Annies na mwamuna wake citiphunzitsa ciani pankhani ya mmene tingacitile ulaliki wa pa kasitandi mogwila mtima?