Mmene Mungacitile Ulaliki Pogwilitsila Nchito Thebulo Kapena Shelufu ya Zofalitsa
Ulaliki wogwilitsa nchito thebulo kapena shelufu ndi njila ina imene ikuthandiza kwambili anthu a mitima yabwino kulandila coonadi. (Yoh. 6:44) Akulu akulimbikitsidwa kupanga makonzedwe a ulaliki wapoyela pa malo amene pamadutsa anthu ambili m’gawo la mpingo wao. Popeza mathebulo kapena mashelufu a zofalitsa saikidwa pamalo amodzi mpaka kalekale, palibe cifukwa copemphela cilolezo kwa olamulila. Ndani ali oyenelela kucita ulalikiwu? Ndi ofalitsa amene ali ndi luso la kuzindikila, khalidwe labwino ndiponso luso la kulankhula bwino. Pansipa pali zimene ofalitsa ayenela kucita ndi zimene sayenela kucita kuti ulaliki umenewu uwayendele bwino.