November 26–December 2
MACHITIDWE 6-8
Nyimbo 124 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mpingo Wacikhristu Watsopano Uyesedwa”: (10 min.)
Mac. 6:1—Zioneka kuti akazi amasiye okamba Cigiriki anali kunyalanyazidwa mu mpingo (bt peji 41 pala. 17)
Mac. 6:2-7—Atumwi anacitapo kanthu kuti athetse vutolo (bt peji 42 pala. 18)
Mac. 7:58–8:1—Mpingo unayamba kuzunzidwa kwambili
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mac. 6:15—Kodi “nkhope [ya Sitefano] inali ngati nkhope ya mngelo” m’lingalilo lotani? (bt peji 45 pala. 2)
Mac. 8:26-30—Kodi Akhristu masiku ano amagwila nchito monga ya Filipo m’njila iti? (bt peji 58 pala. 16)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mac. 6:1-15
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kubwelelako Kaciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno itanilani munthuyo ku misonkhano.
Kubwelelako Kacitatu: (3 min. olo kucepelapo) Sankhani mwekha lemba, na kugaŵila cofalitsa cophunzitsila Baibo.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) lv mape. 33, 34 mapa. 16-17
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Okonzeka Kupeleka Mphatso kwa Yehova”:(15 min.) Nkhani yokambilana yokambiwa na mkulu. Yambani mwa kutambitsa vidiyo yakuti, ‘Kupeleka Mphatso kwa Yehova’. Ŵelengani kalata yocokela ku ofesi ya nthambi yokamba za ciyamikilo pa zopeleka zimene inalandila m’caka catha ca utumiki. Kambilanani mmene timapindulila na zopeleka zathu. Fotokozani mmene mpingo umaseŵenzetsela ndalama mwezi uliwonse. Kambilanani njila zimene tingaseŵenzetse pocita zopeleka komanso mmene zopelekazo zimaseŵenzetsedwela. Yamikilani mpingo cifukwa ca kuwolowa manja pocita zopeleka.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 43 mapa. 19-29
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 67 na Pemphelo