CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 6-8
MpingoWacikhristu Watsopano Uyesedwa
6:1-7; 7:58–8:1
Akazi amasiye okamba Cigiriki amene anali atangobatizika kumene, komanso amene anakhala nthawi yaitali ku Yerusalemu, anali kunyalanyazidwa. Kodi kupanda cilungamo kumeneko kunawakhumudwitsa, kapena anayembekezela pa Yehova kuti iye adzakonza zinthu?
Pambuyo pakuti Sitefano waponyewa miyala, komanso pamene cizunzo coopsa cinacititsa Akhristu a ku Yerusalemu kuthaŵila kumadela a ku Yudeya na ku Samariya, kodi iwo anazilala pa nchito yawo yolalikila?
Cifukwa ca thandizo la Yehova, mpingo watsopano umenewu unapilila ndipo unakula.—Mac. 6:7; 8:4.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimacita bwanji nikakumana na mayeselo?’