CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 4-6
“Cofufumitsa Cacing’ono Cimafufumitsa Mtanda Wonse”
N’cifukwa ciani tingakambe kuti kucotsa munthu mumpingo ni makonzedwe acikondi, popeza cimapweteka mtima?
Kucotsa munthu mu mpingo kumaonetsa kuti . . .
timakonda Yehova, komanso timalemekeza dzina lake.—1 Pet. 1:15, 16
timakonda mpingo pouteteza ku makhalidwe oipa.—1 Akor. 5:6
timakonda wocimwayo cifukwa kumamuthandiza kuzindikila colakwa cake.—Aheb. 12:11
Kodi tingalithandize bwanji banja lacikhristu limene lili na munthu wocotsedwa?