CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 TIMOTEYO 1-4
“Mulungu Sanatipatse Mzimu Wamantha”
1:7, 8
Mawu ouzilidwa amene mtumwi Paulo anauza Timoteyo angatilimbikitse. M’malo mocita manyazi na uthenga wabwino, tingalankhule molimba mtima za cikhulupililo cathu, ngakhale kuti nthawi zina zingacititse kuti ‘timve zowawa.’
Ni pa zocitika ziti pamene nifunika kukhala wolimba mtima?