CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 PETULO 3-5
“Mapeto a Zinthu Zonse Ayandikila”
4:7-9
Posacedwa, tiyang’anizana na cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo padzikoli. Tingacite ciani kuti tikhalebe okhulupilika lomba mpaka m’tsogolo?
Muzipemphela mosalekeza, mwa kuseŵenzetsa mtundu uliwonse wa pemphelo
Kulitsani cikondi canu pa abale na alongo, ndipo pitilizani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi iwo
Muziwaceleza mwacimwemwe
DZIFUNSENI KUTI, ‘Ni njila ziti zimene ningaonetsele kuti ndine wacikondi ndiponso woceleza kwa abale na alongo a m’dela lathu komanso a ku maiko ena?’