LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 October tsa. 8
  • Kampeni Yapadela Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu November

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kampeni Yapadela Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu November
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kampeni Yapadela Yolengeza Ufumu wa Mulungu mu September!
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Lalikilani Uthenga Wabwino Wakuti Dziko Labwino Lili Pafupi!
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Makambilano Acitsanzo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Makambilano Acitsanzo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 October tsa. 8
M’bale na mlongo akukamba ndi anthu pocita ulaliki wa tumasitandi. Pa kasitandi kena pali ‘Nsanja ya Mlonda’ ya Na. 2 2020.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kampeni Yapadela Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu November

‘Nsanja ya Mlonda’ ya Na. 2 2020 yamutu wakuti ‘Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?’

Yesu anali kulengeza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Komanso anaphunzitsa anthu kuti azipemphelela Ufumuwo kuti ubwele. (Mat. 6:9, 10) M’mwezi wa November, tidzakhala na nchito yapadela yolengeza mwakhama za Ufumu wa Mulungu. (Mat. 24:14) Konzani zinthu pa umoyo wanu kuti mukatengeko mbali mokwanila pa kampeni imeneyo. Onse amene adzacita upainiya wothandiza m’mwezi umenewu, adzakhala na ufulu wosankha kulalikila maola 30 kapena 50.

Pocita kampeniyo, mukaŵelenge lemba lokamba za Ufumu wa Mulungu kwa anthu ambili a m’gawo lanu mmene mungathele. Posankha lemba loŵelenga, ganizilani zikhulupililo za anthu a m’gawo lanu. Ngati winawake waonetsa cidwi pa ulendo woyamba, m’gaŵileni Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya Na. 2 2020. Mukatelo, mukabweleleko mwamsanga, ndipo mudzayesetse kuyambitsa phunzilo la Baibo poseŵenzetsa cimodzi mwa zida za mu Thuboksi yathu. Nthawi yangotsala pang’ono kuti Ufumu wa Mulungu uphwanye maboma onse otsutsana nawo. (Dan. 2:44; 1 Akor. 15:24, 25) Conco, tiyeni tiuseŵenzetse mokwanila mwayi wapadela umenewu, poonetsa kuti ndife okhulupilika kwa Yehova na Ufumu wake!

Yesu wakhala pa mpando wacifumu kumwamba, ndipo akulamulila monga Mfumu m’Paradaiso padziko lapansi.

Ufumu wa Mulungu udzabweletsa Paradaiso pa dziko lapansi!

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani