UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Lalikilani Uthenga Wabwino Wakuti Dziko Labwino Lili Pafupi!
M’mwezi wa November, tidzacita zonse zotheka kuti tikalalikile kwa anthu ambili za uthenga wabwino wakuti dziko labwino lili pafupi. (Sal. 37:10, 11; Chiv. 21:3-5) Sinthankoni zinthu zina pa umoyo wanu kuti mukatengeko mbali mokwanila pa kampeni imeneyi. Ngati mudzacitako upainiya wothandiza m’mwezi umenewu, mungasankhe kucita upainiya wa maola 30 kapena 50.
Konzekelani lemba lokamba za dziko latsopano kuti mukaŵelengele anthu ambili mmene mungathele. Posankha lemba lokaŵelenga, ganizilani zimene zingawacititse cidwi anthu a m’gawo lanu. Ngati wina waonetsa cidwi pa ulendo woyamba, mugaŵileni magazini yogaŵila ya Nsanja ya Mlonda ya Na. 2 2021. Ndiyeno, bwelelankoni mwamsanga kuti mukayambitse phunzilo la Baibo pogwilitsila nchito bulosha yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Kugwila nawo mokwanila nchito youza ena “uthenga wabwino wa zinthu zabwino” kumabweletsa cimwemwe cacikulu!—Yes. 52:7.
ONELELANI VIDIYO YA NYIMBO YOPEKEDWA KOYAMBA YAKUTI DZIKO LATSOPANO LIKUBWELALO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
Kodi kamtsikana ka mu vidiyo ya nyimbo imeneyi kakudziyelekezela kuti kali m’dziko lotani?
Ni zinthu ziti za m’dziko latsopano zimene mumaziyembekezela mwacidwi?
Kodi kusinkhasinkha za ciyembekezo canu kungakuthandizeni bwanji kudzatengako mbali mokwanila pa kampeni ya mu November?—Luka 6:45