LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 July tsa. 13
  • Kampeni Yapadela Yoyambitsa Maphunzilo a Baibo mu September

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kampeni Yapadela Yoyambitsa Maphunzilo a Baibo mu September
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Tingagwilitsile Nchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kampeni Yapadela Yolengeza Ufumu wa Mulungu mu September!
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Kugwilitsila Nchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Pophunzitsa
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 July tsa. 13
Zithunzi: Banja limene lili m’nkhani yakuti “Dziikileni Zolinga za Caka ca Utumiki Catsopano—Kucita Upainiya” likulalikila. 1. Mtsikana uja na amayi ake akukambilana na mzimayi m’kabuku kakuti “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya” pakhomo la nyumba yake. 2. Ambuye ake akugwilitsila nchito kabuku kakuti “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya” potsogoza phunzilo pa foni. 3. Atate na amayi ake aimilila m’mbali mwa kasitandi ka ulaliki kamene pali zithunzi za kabuku kakuti “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya.” Pa kasitandiko palinso cithunzi cokhala na mawu odziŵitsa anthu za phunzilo la Baibo laulele.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kampeni Yapadela Yoyambitsa Maphunzilo a Baibo mu September

Mu September, tidzayesetsa kupempha mwininyumba aliyense kuti tiziphunzila naye Baibo poseŵenzetsa kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! M’mweziwu, ofalitsa adzakhala na mwayi wosankha kucita upainiya wothandiza wa maola 30. Kodi tidzacita bwanji kampeni yapadela imeneyi?

  • Pa Ulendo Woyamba: Seŵenzetsani mfundo za pa cikuto cakumbuyo ca kabukuka pokopa cidwi ca munthu, ndipo m’pempheni kuti mumuonetse mmene phunzilo la Baibo limacitikila. Musaiŵale anthu amene anaonetsa cidwi kumbuyoko, kuphatikizapo amene mumacitako maulendo obwelelako. Ngakhale amene kale anali kukana kuphunzila Baibo, mwina angakhale na cidwi na njila yatsopano yophunzilila komanso kabuku katsopano. Simuyenela kusiya tumabuku tumenetu pa nyumba zimene simunapezepo anthu. Komanso musatumize tumabukutu m’makalata amene mwalembela anthu omwe sanaonetsepo cidwi. M’mwezi umenewu, Komiti ya Utumiki ya Mpingo ingawonjezele masiku ena okumana kaamba kotenga malangizo a ulaliki.

  • Mipata Ina: Ngati mpingo wanu umaseŵenzetsa tumasitandi twa ulaliki, muyenela kuonetsa cithunzi ca kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya pa tumasitandito. Munthu akaonetsa cidwi, muuzeni kuti akalandila kabuku kameneka, alinso na mwayi wolandila maphunzilo a Baibo aulele. Kenako muonetseni mwacidule mmene phunzilo la Baibo limacitikila, kapena panganani naye kuti mukamuonetse panthawi ina. Woyang’anila utumiki angapange makonzedwe akuti ofalitsa aluso akalalikile m’gawo lamalonda, na kupempha anthu kuti ayambe kuphunzila nawo Baibo. Mungapemphenso anzanu a kunchito, kapena amene mwakumana nawo pocita ulaliki wamwayi kuti muyambe kuphunzila nawo Baibo.

Yesu anatilamula kupanga ophunzila na ‘kuwaphunzitsa.’ (Mat. 28:19, 20) Pemphelo lathu n’lakuti kampeni yapadelayi itithandize kukwanilitsa udindo umenewu pogwilitsila nchito cofalitsa cimeneci cakuti Kondelani na Moyo Kwamuyaya!

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani