LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 December tsa. 8
  • Pitilizani Kugaŵila Magazini

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pitilizani Kugaŵila Magazini
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Ndani Angacite Nazo Cidwi Izi?
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 December tsa. 8
Mlongo akukambilana na mayi nkhani inayake ya mu ‘Galamuka!’

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pitilizani Kugaŵila Magazini

Kuyambila mu 2018, magazini iliyonse yogaŵila imafotokoza pa nkhani imodzi cabe. Magazini onsewa ni mbali ya zida zophunzitsila za mu Thuboksi yathu. Conco tiyenela kuwaseŵenzetsa mu ulaliki. Komanso tinganyamuleko magazini angapo ngati tili pa ulendo kapena popita kukagula zinthu. Colinga ca magaziniwa si kutsogozela phunzilo la Baibo. Ngakhale n’conco, angapangitse munthu kukhala na cidwi na uthenga wathu.

Mukayambitsa makambilano, ŵelengani lemba na kuchula nkhani ya m’magazini imene munthuyo angacite nayo cidwi. Mwacitsanzo, ngati ali na ŵana kapena ali na cisoni kapena nkhawa, mungakambe kuti: “Posacedwapa, n’naŵelengapo nkhani inayake yothandiza pa mbali imeneyi. Kodi mungakonde kuiona?” Ngati munthuyo waonetsa cidwi, mungamugaŵile magazini yopulintidwa kapena mungamutumizile pa foni kapena pa tabuleti yake. Mungacite zimenezi olo kuti ni ulendo woyamba. Ngakhale kuti colinga cathu cacikulu si kugaŵila zofalitsa, kugaŵila magazini kungatithandize kupeza anthu amene amafuna kucita zimene aphunzila.—Mac. 13:48.

2018

Zithunzi: Mitu ya magazini a 2018 a ‘Nsanja ya Mlonda’ yogaŵila na ‘Galamuka!’ 1. ‘Kodi Baibo Ikali Yothandiza Masiku Ano?’ 2. ‘Kodi Kutsogolo Kuli Ciani?’ 3. ‘Kodi Mulungu Amakudelani Nkhawa?’ 4. ‘Njila Yopezela Cimwemwe.’ 5. ‘Zinsinsi 12 za Mabanja Acimwemwe.’ 6. ‘Thandizo Kwa Ofedwa.’

2019

Zithunzi: Mitu ya magazini a 2019 a ‘Nsanja ya Mlonda’ yogaŵila na ‘Galamuka!’ 1. ‘Kodi Mulungu N’ndani?’ 2. ‘Kodi Moyo Ukali na Phindu kwa Ine?’ 3. ‘Kodi Moyo Ni Uno Cabe Umene Ulipo?’ 4. ‘Kodi Zidzatheka Kukhala Mwamtendele ndi Motetezeka pa Dzikoli?’ 5. ‘Zinthu 6 Zimene Ana Afunika Kuphunzila.’ 6. ‘Kodi Baibo Ingakuthandizeni Kukhala na Umoyo Wabwino?’

2020

Zithunzi: Mitu ya magazini a 2020 a ‘Nsanja ya Mlonda’ yogaŵila na ‘Galamuka!’ 1. ‘Kufuna-funa Coonadi.’ 2. ‘Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?’ 3. ‘Madalitso Osatha Ocokela Kwa Mulungu Wacikondi.’ 4. ‘Pezani Thandizo pa Nkhawa Zanu.’ 5. ‘Mafunso 5 Pankhani ya Mavuto Ayankhidwa.’ 6. ‘Kodi Kuli Mankhwala Othetsela Tsankho?’

Kodi anthu m’gawo lanu amacita cidwi na nkhani ziti?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani