CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzikwanilitsa Malumbilo Anu
Aisiraeli anali kupanga malumbilo mwa kufuna kwawo, koma akalumbila anali kufunika kukwanilitsa (Num. 30:2; it-2 1162)
Malumbilo angaphatikizepo kudziletsa ngakhale pa zinthu zimene si zolakwika (Num. 30:3, 4; w17 04 3¶2)
Nkhani ya malumbilo masiku ano imakhala pakati pa Yehova na wolambila aliyense payekha (Num. 30:6-9; w04 8/1 27 ¶3)
Malumbilo aŵili ofunika kwambili amene Mkhristu angapange masiku ano ni lumbilo la kudzipatulila kwa Mulungu komanso la cikwati.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nikuyesetsa kukwanilitsa malumbilo amene n’napanga?’