CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mukapitikitse Anthu Onse a m’Dzikolo”
Yehova analamula anthu ake kuti akacotse ciliconse m’Dziko Lolonjezedwa cimene cikanawacititsa kuphwanya malamulo ake (Num. 33:52; w10 8/1 23)
Yehova anawalonjeza kuti adzawadalitsa ngati adzalimbika kulanda dziko lonse la Kanani (Num. 33:53)
Aisiraeli anacenjezedwa kuti adzakumana na mavuto ngati sadzagonjetsa adani awo onse (Num. 33:55, 56; w08 2/15 27 ¶5-6; it-1 404 ¶2)
Kuti tikondweletse Yehova, tiyenela kupewelatu mcitidwe ulionse wodetsedwa, umene ungawononge ubale wathu na iye. (Yak. 1:21) Yehova amatipatsa mphamvu zotithandiza kugonjetsa macitidwe aucimo na kupewa mzimu woipa wa dzikoli.